Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Ofesi ya Nthambi ya Mboni za Yehova ku Bishkek, Kyrgyzstan

23 DECEMBER, 2021
KYRGYZSTAN

Komiti Yoona za Ufulu wa Anthu Yanena Kuti Boma la Kyrgyzstan Linaphwanyira a Mboni za Yehova Ufulu

Komiti Yoona za Ufulu wa Anthu Yanena Kuti Boma la Kyrgyzstan Linaphwanyira a Mboni za Yehova Ufulu

Komiti ya Bungwe la United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu (CCPR) yopangidwa ndi anthu 15, inadzudzula boma la Kyrgyzstan chifukwa chophwanya ufulu wa Mboni za Yehova woti azipembedza m’zigawo zitatu za dzikoli. M’chikalata chamasamba 7 chomwe komitiyi inatulutsa, chinanena kuti boma la Kyrgyzstan liyenera kupereka “chipukuta misozi chokwanira” kwa a Mboni za Yehova komanso kuti ayenera “kutsatira ndondomeko zonse zoyenera kuti nkhani zophwanyira anthu ufulu ngati zimenezi zisadzachitikenso.” Ndipo uwu ndi ulendo wachiwiri kuti komitiyi idzudzule boma la Kyrgyzstan chifukwa chophwanya ufulu wa a Mboni za Yehova.

Gulu loyamba la a Mboni za Yehova za ku Kyrgyzstan linalembedwa m’kaundula wa boma m’chaka cha 1993 ndipo a Mboni za Yehova analembedwa monga gulu lodziwika m’dziko lonselo m’chaka cha 1998. Kwa zaka zambiri, Amboni m’dziko lonse la Kyrgyzstan akhala akupembedza mwaufulu. Komabe kwa zaka zopitirira 10 tsopano, Komiti ya Boma Yoona Nkhani Zachipembedzo (SCRA), yakhala ikukana kulemba m’kaundula wake magulu ena atatu a Mboni za Yehova opezeka m’madera a Osh, Naryn, ndi Jalal-Abad a m’chigawo chakum’mwera cha dzikoli. Komitiyi yakhala ikukana kulemba maguluwa ngakhale kuti abale akhala akuipempha mobwerezabwereza. Chifukwa chokana pempholi abale ndi alongo alibe mwayi wopembedza mwaufulu, kuchita misonkhano ya mpingo komanso ikuluikulu. Alibenso ufulu wokhala ndi malo opembedzera. Choncho Komiti ya Bungwe la United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu inapeza kuti boma la Kyrgyzstan likusala a Mboni za Yehova m’madera atatuwa chifukwa cha zomwe amakhulupirira.

Komiti ya Bungwe la United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu ikuyembekezera kuti akuluakulu a boma la Kyrgyzstan, atsatira “ndondomeko zonse zoyenera kuti nkhani zophwanyira anthu ufulu ngati zimenezi zisadzachitikenso.” Boma la Kyrgyzstan lapatsidwa masiku 180 oti lifotokozere Komiti ya Bungwe la United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu, zomwe achitapo potsatira zomwe komitiyi inanena.

Sitikudziwa ngati akuluakulu a boma la Kyrgyzstan angatsatire zomwe anauzidwazi ndi kulola kuti abale ndi alongo athu okhala m’madera atatuwa akhale ndi ufulu wotsatira zomwe amakhulupirira. Komabe, akatswiri oona za ufulu wa anthu akhala akutsatira nkhaniyi mwachidwi ndipo atulutsa lipoti lonena kuti Komiti ya Boma Yoona Nkhani Zachipembedzo “ ku Kyrgyzstan ikunyalanyaza chigamulo cha Bungwe la United Nations chomwe chinapangidwa mu 2019.”

Kaya boma la Kyrgyzstan litsatira malangizo a Bungwe la United Nations kapena ayi, tikudziwa kuti Yehova akudziwa bwino zomwe abale ndi alongo athu ku Kyrgyzstan akukumana nazo. (Salimo 37:18) Atate wathu wachikondi apitiriza kuwadalitsa chifukwa cha khama ndi kukhulupirika kwawo.—Salimo 37:28.