24 APRIL, 2015
MEXICO
Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la Chinenero cha Chitsotsilu Linatulutsidwa ku Mexico
MEXICO CITY—A Mboni za Yehova anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu mu Chitsotsilu pa msonkhano womwe unachitika pa 26 mpaka 28 December, 2014. Msonkhanowu unachitikira mumzinda wa Tuxtla Gutierrez, ku Chiapas. Mutu wa msonkhanowu unali wakuti, “Pitirizani Kufunafuna Ufumu wa Mulungu Choyamba” ndipo nkhani zake zinakambidwa m’chinenero cha Chitsotsilu chomwe chimayankhulidwa ndi anthu enaake otchedwa Amaya. Anthu enanso anamvetsera msonkhanowu mumzinda wa Comitan, ku Chiapas komweko. Kuwonjezera pa Baibulo lomwe linatulutsidwali, anthu onse omwe anabwera pamsonkhanowu, okwana 5,073, analandira mabuku komanso zinthu zina za m’chinenerochi.
Woyankhula m’malo mwa a Mboni za Yehova ku Mexico, dzina lake Gamaliel Camarillo anati: “Tasangalala kwambiri ndi kutulutsidwa kwa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu m’chinenero cha Chitsotsilu. Tikuyembekezera kuti tizigwiritsa ntchito Baibuloli tikamakambirana ndi anzathu mfundo zochokera m’mawu a Mulungu.”
Bungwe lina loona za maphunziro la ku Mexico linanena kuti anthu oposa 350,000 ndi omwe amayankhula chinenerochi. Ena mwa anthuwa amakhala ku Baja California, Campeche, Chiapas, Oaxaca komanso ku Veracruz. Pofuna kuthandiza anthu amenewa, a Mboni za Yehova anakhazikitsa ofesi yomasulira mabuku m’chinenerochi m’tauni ya San Cristobal de las Casas ku Chiapas. Pa ofesiyi pali anthu okwana 15 ndipo amamasulira mabuku m’Chitsotsilu. Panopa a Mboni za Yehova ali ndi mabuku, timapepala komanso zinthu zina za m’chinenerochi zokwana 60, ndipo chinthu choyamba chomwe anamasulira chinatuluka mu 2002. Zinthu zimenezi zikupezekanso pa webusaiti yathu ya jw.org ndipo mukhoza kuzipanga dawunilodi.
Yankhulani ndi:
Kuchokera M’mayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000
Mexico: Gamaliel Camarillo, tel. +52 555 133 3048