Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pamwamba, kuyambira kumanzere kupita kumanja: M’bale Vyacheslav Boronos, Saveliy Gargalyk, Yevgeniy Kayryak ndi M’bale Artem Kim. Pansi: M’bale Sergey Loginov, Aleksey Plekhov ndi M’bale Sergey Volosnikov

26 JULY, 2022
RUSSIA

Anapeza Mphamvu Pogwiritsa Ntchito Pemphero

Anapeza Mphamvu Pogwiritsa Ntchito Pemphero

Posachedwa khoti la Mzinda wa Surgut m’Dera la Khanty-Mansi Autonomous Area—Yugra, lipereka chigamulo chake pa mlandu wa abale 17 ndi mlongo mmodzi. Pa gululo pali M’bale Vyacheslav Boronos, Saveliy Gargalyk, Yevgeniy Kayryak, Artem Kim, Sergey Loginov, Aleksey Plekhov komanso M’bale Sergey Volosnikov. Loya waboma sananene chilango chomwe akufuna kuti anthuwa apatsidwe.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

  1. 15 February, 2019

    Apolisi anakafufuza zinthu m’nyumba zambiri za Mboni za Yehova ku Surgut ndi m’mizinda ina yapafupi. Pamapeto pake, abale atatu kuphatikizapo Sergey Loginov anakatseredwa kundende poyembekezera kuwazenga mlandu. Pambuyo pake m’bale wina anauzidwa kuti apite kuchipatala cha anthu ovutika maganizo. Abale 7 omwe atchulidwa munkhaniyi anamenyedwa ndi apolisi chifukwa choti anakana kuulula Akhristu anzawo

  2. 26 February, 2019

    Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linalamula boma la Russia kuti litulutse m’ndende Sergey Loginov kuti akalandire chithandizo kuchipatala

  3. 11 April, 2019

    Sergey Loginov anatulutsidwa m’ndende

  4. 29 October, 2021

    Mlandu unayamba kuzengedwa

Zokhudza Anthuwa

Pomwe abale athu akupitiriza kukumana ndi mayesero, tili ndi chikhulupiriro chonse kuti Yehova akumva mapemphero awo komanso kuwayankha mwamsanga pomwe akufunikira kwambiri thandizo lake.—Salimo 69:17.