1 MAY 2023
RUSSIA
“Mavuto Anga Ndi Osakhalitsa”
Posachedwapa, Khoti la m’boma la Urupskiy lomwe lili ku Karachayevo-Circassian Republic lilengeza chigamulo chake pa mlandu wokhudza Mlongo Irina Perefileva. Loya woimira boma pamlanduwu akuyembekezereka kunena chilango chimene akufuna kuti chiperekedwe kwa mlongoyu.
Zokhudza Mlongoyu
Mofanana ndi Mlongo Irina, timatonthozedwa kudziwa kuti ngakhale mavuto amene tikukumana nawo angaoneke ngati ovuta kuwapirira, koma “ndi akanthawi ndiponso aang’ono” tikawayerekezera ndi madalitso amene Yehova wasungira atumiki ake okhulupirika m’tsogolomu.—2 Akorinto 4:17.
Nthawi ndi Zochitika
9 January 2021
Anachita chipikisheni m’nyumba yawo
22 November 2021
Anamutsegulira mlandu
23 November 2021
Anachitanso chipikisheni m’nyumba mwawo
29 November 2021
Anauzidwa kuti ali ndi mlandu wochita zinthu ndi gulu loopsa
15 October 2022
Analetsedwa kuchita zinthu zina
6 December 2022
Mlandu unayamba kuzengedwa