Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Artur Lokhvitskiy ndi mkazi wake Anna

26 JANUARY 2021
RUSSIA

M’bale Artur Lokhvitskiy Akhoza Kugamulidwa Kuti Akakhale M’ndende Zaka 4 Pambuyo Pochita Zipikisheni ku Birobidzhan

M’bale Artur Lokhvitskiy Akhoza Kugamulidwa Kuti Akakhale M’ndende Zaka 4 Pambuyo Pochita Zipikisheni ku Birobidzhan

Tsiku Lopereka Chigamulo

Pa 2 February 2021, a Khoti la m’Boma la Birobidzhan lomwe lili m’dera loima palokha la Ayuda ku Russia, lidzalengeza chigamulo chake pa mlandu wokhudza M’bale Artur Lokhvitskiy. M’baleyu akhoza kugamulidwa kuti akakhale m’ndende zaka 4.

Zokhudza M’baleyu

Artur Lokhvitskiy

  • Chaka chobadwa: 1986 (Ku Belgorodskoye, M’dera Loima Palokha la Ayuda ku Russia)

  • Mbiri yake: Bambo awo anamwalira iwowa ali ndi zaka 7 zakubadwa. Anaphunzira ntchito zamagetsi komanso anakhala katswiri woteteza kuti moto usabuke. Analandira ziwongola dzanja zambiri chifukwa chogwira ntchito mwakhama.

    A Lokhvitskiy anayamba kuphunzira kukonda Yehova ali aang’ono ndipo ankawaphunzitsa ndi mayi awo. Mu 1998, anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova ali ndi zaka 11. Mu 2018, anakwatirana ndi Anna. Awiriwa amakonda kuyenda m’madera osiyanasiyana komanso kucheza ndi kuchita zinthu zina panja

Mlandu Wake

Mu May 2018, atangotha miyezi itatu m’banja, apolisi anachita chipikisheni m’nyumba ya M’bale ndi Mlongo Lokhvitskiy. Apolisiwo anatchula ulendo wochita zipikisheniwu kuti “Tsiku Lachiweruzo,” ndipo pa tsikuli apolisi 150 anachita zipisheni m’nyumba 22 za a Mboni za Yehova. Apolisiwa anachitanso chipikisheni m’nyumba ya Mlongo Irina omwe ndi mayi awo a M’bale Lokhvitskiy. Pa 31 July 2019, apolisi a gulu la chitetezo la FSB ku Birobidzhan anayamba kuimba mlandu M’bale Lokhvitskiy womuganizira kuti amachita nawo zinthu zoopsa. Anna komanso Mlongo Irina nawonso akuimbidwa milandu ina.

Milandu imene banjali likuimbidwa ikuchititsa kuti zizikhala zovuta kuti apeze ndalama zokwanira zogulira zinthu zofunika. Apolisi akumaletsanso M’bale Lokhvitskiy kutenga ndalama ku akaunti yake ya kubanki. Kuonjezera apa, bwana wa M’baleyu wamuopseza kuti akhoza kumuchotsa ntchito.

Banjali silikuthanso kuchita zinthu ngati kale chifukwa apolisi akufufuzabe milandu yawo. M’bale Lokhvitskiy akuti: “Panopa moyo wathu wasintha kwambiri. Sitingathenso kukonza zoti mlungu uno (kapena lero) tipanga zotani. [Apolisi] amatiuza kuti tipite kuofesi yawo pa nthawi zosiyanasiyana mmene afunira. Zimenezi zimachititsa kuti zonse zomwe tinakonza kuti tipange pa tsikulo zizilephereka.”

M’bale Lokhvitskiy ndi mkazi wake akuthokoza kwambiri chifukwa cha zimene abale ndi alongo amawachitira powathandiza. M’bale Lokhvitskiy akuti: “Abale ndi alongo amatilimbikitsa kwambiri komanso amatithandiza kukhala odekha ndiponso kuti tikhalebe pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. . . . Sitingathe kufotokoza chimwemwe chomwe tili nacho chifukwa chokhala m’gulu la Yehova komanso mwayi umene tili nawo woteteza dzina la Yehova m’makhoti. N’zoonekeratu kuti Yehova sasiya anthu ake.”

Banjali limachita zinthu molimba mtima ndiponso limalimbikitsidwa kwambiri chifukwa chakuti nthawi zonse limachita zinthu zokhudza kulambira. Koma sikuti likudutsa moyera. Mwachitsanzo, M’bale Lokhvitskiy akufotokoza zomwe zinachitika pambuyo pa chipikisheni chomwe apolisi anachitchula kuti “Tsiku Lachiweruzo.” Iye anati: “Tinalibe Baibulo ngakhalenso buku lina lililonse lotithandiza kuphunzira Baibulo.” Poyamba zimenezi zinamudetsa nkhawa kwambiri m’baleyu. Sankadziwa zomwe angachite kuti iye ndi banja lake apitirize kuchita zinthu zokhudza kulambira. Koma anakumbukira mfundo yofunika kwambiri yakuti: “[Gulu la FSB] silikanatha kutilanda mwayi wopemphera kwa Yehova womwe tili nawo. Choncho nthawi yomweyo tinapemphera kwa Yehova. Pemphero ndi limene linatithandiza kwambiri.”

Yehova anayankha mapemphero awo mofulumira ndipo anawapatsa chakudya chauzimu chomwe ankafunikira kuti ayambirenso kuchita zinthu zokhudza kulambira. M’bale Lokhvitskiy anati: “Sitiphonya kuchita kulambira kwa pabanja, kukonzekera misonkhano ndiponso kuwerenga Baibulo limodzi monga banja. Sikuti zimenezi zangotithandiza kuti tizigwirizana monga banja basi, koma zatithandizanso kuti tiziona dzanja la Mulungu pa moyo wathu komanso kuti tiziona zinthu moyenera nthawi zonse.”

Kuonjezera pa kuwerenga ndi kuphunzira Mawu a Mulungu, kuganizira kwambiri madalitso omwe adzalandire m’tsogolo n’kumene kwawathandizanso kwambiri. M’bale Lokhvitskiy akuti: “Tinayamba kuganizira kwambiri za madalitso amene tikuyembekezera m’tsogolo n’kumadziyerekezera tili m’dziko latsopano. Tikufuna kudzagwira nawo ntchito yoyeretsa dzikoli kenako ntchito yomanga. Zimenezi zimatipatsa mphamvu komanso kutilimbikitsa kwambiri.”

Pamene akuyembekezera nthawi imeneyi, m’bale ndi mlongoyu amaganizira kwambiri lemba la Aheberi 13:6 lomwe limati: “Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?” M’bale Lokhvitskiy akuti: “Mfundo yomwe imatilimbikitsa kwambiri ndi yakuti ngakhale kuti talandidwa ufulu wochita zinthu monga kusonkhana pamodzi komanso kuchitira zinthu limodzi monga banja, komabe palibe amene angatilande zinthu zofunika kwambiri zomwe ndi ubwenzi wathu ndi Yehova, pemphero ndiponso madalitso amene tikuyembekezera m’tsogolo.

a Tsikuli likhoza kusintha.