2 APRIL, 2021
RUSSIA
Mlongo Anastasiya Guzeva Akhoza Kumangidwa Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira
Tsiku Lopereka Chigamulo
Posachedwapa khoti la m’M’boma la Birobidzhan lomwe lili m’dera loima palokha la Ayuda lidzapereka chigamulo pa mlandu wa Mlongo Anastasiya Guzeva. a
Zokhudza Mlongoyu
Anastasiya Guzeva
Chaka chobadwa: 1979 (ku Birobidzhan)
Mbiri yake: Analeredwa ndi mayi ake okha ndipo ali ndi azichimwene ake awiri. Ali mwana ankakonda kuwerenga, kuchita masewera komanso kuvina. Ali ndi zaka 10 anapeza Baibulo kunyumba kwa agogo ake. Zimenezi zinamulimbikitsa kuti ayambe kuphunzira za Mulungu. Kenako iye ndi mayi ake anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Onse anabatizidwa mu 1995. Ndipo mu 2001 anakwatiwa ndi Konstantin
Mlandu Wake
M’mwezi wa May 2018 apolisi ku Russia anapita kunyumba ya M’longo Anastasiya ndi M’bale Konstantin. Kenako mu July 2019 apolisi anatsegulira Konstantin mlandu woti amachita zinthu zoopsa ndipo mu February 2020 Anastasiya anamutseguliranso mlandu womwewu. Panopa a Mboni za Yehova okwana 23 awatsegulira milandu yokwana 19 m’dera loima palokha la Ayuda limeneli.
Ofufuza za mlanduwu asokoneza kwambiri moyo wa Anastasiya ndi Konstantin. Mwachitsanzo, iwo anakakamizidwa kuti asiye ntchito pa kusukulu ina yophunzitsa luso loimba chifukwa cha mlandu umene akuwaimbawu. Mu February 2021, Konstantin anagamulidwa kuti wamangidwa kwa zaka ziwiri ndi hafu koma sakalowa kundende panopo.
Anastasiya anafotokoza zimene zamuthandiza kuti apirire. Iye anati: “Ndi bwino kumakumbukira kuti tsiku lina tidzazunzidwa ndipo tiziganizira zimene tingadzachite pa nthawi yovutayo. Mwachitsanzo, tikamawerenga zimene zinachitika pa tsiku lomaliza la moyo wa Yesu padzikoli, titha kuona kuti iye anaganiziratu zimene adzachite akadzamangidwa . . . nthawi yoti adzalankhule, nthawi yokhala chete komanso zoti adzalankhule.”
Anastasiya ananena kuti panopa akumvetsa bwino kwambiri mawu a pa Aroma 8:38, 39. Iye anati: “Mfundo ya pa lemba limeneli ndi yosangalatsa kwambiri. Olamulira akuluakulu m’chilengedwe chonsechi amandikonda kwambiri ndipo palibe chimene chingawalepheretse kundikonda. Mfundo imeneyi imandithandiza kwambiri kuti ndipirire komanso ndilimbe mtima.”
a Nthawi zina deti lenileni lopereka chiweruzo silidziwika