Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kumanzere: Mlongo Marina Chaplykina. Kumanja: M’bale Valeriy Maletskov ndi mkazi wake Marina

18 AUGUST, 2022
RUSSIA

Tinasiya Kuopa Kuzunzidwa Chifukwa Chokhulupirira Yehova

Tinasiya Kuopa Kuzunzidwa Chifukwa Chokhulupirira Yehova

Posachedwa Khoti la m’Boma la Novosibirsk m’Chigawo cha Novosibirsk lipereka chigamulo pa mlandu wa M’bale Valeriy Maletskov ndi Mlongo Marina Chaplykina. Loya wa boma sananene chilango chomwe akufuna kuti khoti lipereke kwa m’bale ndi mlongoyu.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

  1. 2018

    Munthu wina yemwe ankaphunzira Baibulo komanso kupezeka pamisonkhano ya Mboni za Yehova ntchito yathu isanaletsedwe, anayamba kugwirizana ndi apolisi a FSB ku Novosibirsk n’kumawauza zokhudza anthu amene ankapezeka pamisonkhanoyo

  2. 19 April, 2019

    Mogwirizana ndi zomwe anauzidwa, apolisi anakafufuza zinthu m’nyumba 6 za a Mboni za Yehova ku Novosibirsk. Kenako M’bale Maletskov ndi Mlongo Chaplykina anawatsegulira mlandu. Pambuyo pake anakawatsekera m’ndende poyembekezera mlandu

  3. 21 April, 2019

    Anawatulutsa m’ndende. M’bale Maletskov anamuika pa ukaidi wosachoka panyumba ndipo Mlongo Chaplykina anamulamula kuti asapange ulendo uliwonse wochoka m’deralo

  4. 21 February, 2022

    M’bale Maletskov anaimbidwa mlandu wotsogolera gulu lochita zinthu zoopsa. Mlongo Chaplykina anaimbidwa mlandu wothandizira komanso kuchita nawo zinthu za gulu loopsa

  5. 30 March, 2022

    Mlandu unayamba kuzengedwa

Zokhudza Anthuwa

Kupirira kwa anthu amene akulolera kuzunzidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo, ndi umboni wakuti Yehova akuwateteza komanso kuwadalitsa.—1 Yohane 5:4.