18 OCTOBER 2024
RUSSIA
“Yehova Adzandifupa”
Khoti la m’Boma la Vyselkovskiy lomwe lili m’Chigawo cha Krasnodar, posachedwapa lipereka chigamulo chake pa mlandu wa Mlongo Vasilina Penskaya. Loya woimira boma pa mlanduwu sananene chigamulo chimene akufuna kuti Mlongo Penskaya alandire.
Zokhudza Mlongoyu
Timasangalala kudziwa kuti Yehova amachita chidwi ndi mtumiki wake aliyense amene akuzunzidwa ndipo amamutsimikizira kuti ‘adzamupatsa mphoto pa ntchito yake.’—Yeremiya 31:16.
Nthawi Komanso Zimene Zinachitika
13 February 2022
Anachita chipikisheni m’nyumba yawo
23 May 2023
Anamutsegulira mlandu. Ankamuimba mlandu wakuti amakambirana zokhudza Baibulo ndi anthu ena komanso amapezeka nawo pamisonkhano ya chipembedzo cha Mboni za Yehova yomwe imachitika mwamtendere. Ma akaunti ake a kubanki anatsekedwa
18 July 2023
Analetsedwa kupita m’madera ena
31 January 2024
Mlandu wake unayamba kuzengedwa