24 MARCH, 2022
RUSSIA
Yehova Akuthandiza Mabanja a Anthu 6 Omwe Ali M’ndende Podikira Kuzengedwa Kwa Mlandu Wawo
Posachedwa, Khoti la Rostov-on-Don lomwe lili m’Boma la Leninskiy lipereka chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Aleksey Dyadkin, Aleksey Goreliy, Nikita Moiseyev, Vladimir Popov, Yevgeniy Razumov ndi M’bale Oleg Shidlovskiy. Loya woimira boma sananene chigamulo chomwe akufuna kuti abalewa apatsidwe.
Nthawi Komanso Zimene Zinachitika
8 August, 2020
Apolisi a FSB anakafufuza zinthu m’nyumba 17 za Mboni za Yehova m’mizinda itatu ya m’Chigawo cha Rostov komanso mumzinda wa Kursk. M’bale Goreliy, Moiseyev, Razumov ndi M’bale Shidlovskiy, anamangidwa ndipo tsiku lotsatira anakawatsekera m’ndende podikira kuzengedwa kwa mlandu wawo. M’bale Popov anaikidwa pam’ndandanda wa anthu omwe boma likuwafuna kwambiri.
12 August, 2020
Apolisi a FSB anamanga M’bale Popov ndipo pambuyo pa masiku awiri, anamupititsa kundende kuti azikayembekezera kuzengedwa kwa mlandu wake.
21 August, 2020
M’bale Dyadkin atapita kupolisi kuti akayankhe mafunso, anatumizidwa kundende kuti azikayembekezera kuzengedwa mlandu
28 June, 2021
Loya anapita kundende kukakumama ndi abalewa. Anamufotokozera mavuto omwe akukumana nawo komanso kuti m’maselo mukumakhala mozizira kwambiri mpaka kufika madigirii 40 moti m’makoma mukumakhala mungu ndipo akaidi akupatsirana COVID-19
21 July, 2021
M’bale Popov anapezeka ndi vuto lolephera kupuma ndipo anapita naye pakachipatala ka ndende ina. Kenako anamutumiza kuchipatala chachikulu
30 September, 2021
Pambuyo pokhala m’chipatala kwa miyezi iwiri, M’bale Popov anabwerera nayenso kundende
17 November, 2021
Mlandu unayamba kuzengedwa ndipo abale onse 6, anapitirizabe kuwasunga kundende
Zokhudza Abalewa
Tikupitiriza kupemphera kwa Yehova kuti athandize abale athuwa limodzi ndi mabanja awo. Tili ndi chikhulupiriro kuti Yehova apitiriza kuwapatsa mphamvu komanso kuwathandiza kukhalabe ndi chikhulupiriro.—Aroma 15:30.