28 JULY, 2022
RUSSIA
Yehova Wandipatsa Anzanga Odalirika Omwe Amandithandiza
Posachedwapa, Khoti la Oktykabrskiy lomwe lili m’boma la Novosibirsk, lipereka chigamulo chake pa mlandu wokhudza M’bale Aleksandr Seredkin. Loya woyimira boma sananene chilango chimene akufuna kuti m’baleyu apatsidwe.
Nthawi Komanso Zimene Zinachitika
19 April, 2019
Anamutsegulira mlandu
21 April, 2019
Anaikidwa pa ukayidi wosachoka panyumba
8 May, 2019
Anamulemba pa mndandanda wa anthu ochita zauchigawenga
2 March, 2022
Anayamba kuzengedwa mlandu
Zokhudza M’baleyu
Tikusangalala kuti abale ndi alongo athu akupitirizabe “kutonthozana ndi kulimbikitsana” kuti Yehova apitirize kulemekezedwa.—1 Atesalonika 5:11