MAY 10, 2018
RUSSIA
Khoti la ku Oryol Limvetsera Umboni Koyamba pa Mlandu wa a Dennis Christensen
Pa 23 April, 2018 khoti laling’ono mumzinda wa Zheleznodorozhniy ku Oryol linapitiriza kuzenga mlandu wa a Dennis Christensen. Bambo Christensen ndi nzika ya dziko la Denmark komanso ndi a Mboni za Yehova. Iwo anamangidwa mu May 2017 ali pamsonkhano wa chipembedzo chawo ndipo akhala akusungidwa m’ndende kuchokera pa nthawi imeneyo.
Woimira boma pa milandu bambo Fomin, ananena kuti bambo Christensen anapalamula mlandu ‘wotsogolera zochita za gulu lomwe limachita zinthu zoopsa’ lomwe ndi Bungwe Loimira Mboni za Yehova ku Oryol limene linatsekedwa mu June 2016 polinamizira kuti linachita zinthu zoopsa. Maloya a bambo Christensen anakana mlanduwu chifukwa mpingo wa Mboni za Yehova ku Oryol si bungwe loimira Mboni za Yehova koma langokhala gulu la anthu amene amalambira Mulungu mwamtendere ndipo amakumana pamodzi n’kumaphunzira Baibulo. Maloyawa anatsindika kuti akuluakulu a boma la Russia ananena okha kuti sanaletse chipembedzo cha Mboni za Yehova komanso kuti buku la malamulo a dziko la Russia limasonyeza kuti munthu aliyense ali ndi ufulu wochita zinthu zimene amakhulupirira pa nkhani ya chipembedzo. a Choncho pamene bambo Christensen anapezeka pa msonkhano wa chipembedzo, ankangochita zomwe amakhulupirira basi.
Anthu anayamba kupereka umboni wawo pa nkhaniyi pa 24 April, 2018. Munthu woyamba amene woimira boma pa milandu anamuitana kuti apereke umboni anali woimira apolisi a gulu lina loona za chitetezo. (Federal Security Service) Munthuyo anafotokoza kuti wakhala akujambula vidiyo ya zinthu zomwe zimachitika pa Nyumba ya Ufumu ku Oryol kuyambira mu 2017. Komabe, sanathe kufotokoza zomwe zinkachitika m’Nyumba ya Ufumuyo, chifukwa choti zimene anajambulazo zimangosonyeza bambo Christensen akupereka moni kwa anthu omwe ankalowa m’nyumbayo. Kenako woimira boma pa milandu uja anaitana mzimayi wina yemwe anakasonkhanapo ndi a Mboni za Yehova ku Oryol. Komabe, iye analephera kufotokoza chilichonse pa zimene a Christensen anachita chifukwa choti anapita kumisonkhanoyo bungwe loimira Mboni za Yehova ku Oryol lisanathetsedwe.
Tsiku lotsatira, woimira boma pa milandu anaitana mayi wina wa zaka 78 yemwe ndi wa Mboni za Yehova kuti amufunse mafunso. Woimira boma pa milandu anafunsa mayiwo mafunso kwa maola awiri ndi hafu omwe cholinga chake chinali kungofuna kupangitsa mayiwo kupereka umboni wosonyeza kuti a Christensen anali wolakwa. Koma mayiwo anangofotokoza kuti a Mboni alibe atsogoleri komanso kuti akamachita misonkhano yawo, sagwiritsa ntchito mabuku omwe ndi oletsedwa m’dziko la Russia.
Kuzenga mlanduwu kudzapitirira pa 14 May, 2018, ndipo kukuyembekezeka kupitirira kwa masiku angapo m’mwezi wa May. Ngati angapezeke olakwa, bambo Christensen akhoza kugamulidwa kuti akakhale m’ndende kwa zaka 6 mpaka 10. A Mboni za Yehova padziko lonse akuda nkhawa ndi zimenezi komanso ndi okhudzidwa ndi mavuto omwe a Christensen komanso akazi awo a Irina angakumane nawo.
a Pogwirizana ndi chigamulo choti bungwe loimira Mboni za Yehova lithetsedwe ku Oryol, Khoti Lalikulu Kwambiri linati: “Mamembala a Mboni za Yehova salandidwa ufulu wochita zinthu zogwirizana ndi chipembedzo chawo, popeza kuti n’zotheka kuti azichita zinthu zokhudza kulambira paokha zomwe sizikuphatikizapo kugawira mabuku a chipembedzo omwe ndi oopsa.”