Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Magazini a Nsanja ya Olonda akhala akupeza m’Chizulu kwa zaka zoposa 70

1 FEBRUARY 2024
SOUTH AFRICA

Kulengeza Ufumu wa Yehova mu Chizulu kwa Zaka 75

Kulengeza Ufumu wa Yehova mu Chizulu kwa Zaka 75

Pofika mu January 2024, tinakwanitsa zaka 75 chiyambireni kufalitsa magazini a Nsanja ya Olonda mu Chizulu. Magazini a Nsanja ya Olonda a Chizulu anayamba kusindikizidwa mu 1949 ku ofesi ya nthambi ya South Africa pogwiritsa ntchito makina ochita kupukusa ndi manja. Patapita nthawi, ofesi ya nthambi inapeza makina amakono osindikizira ndipo zimenezi zinathandiza kuti azisindikiza magazini ochuluka komanso ooneka bwino.

Womasulira m’zaka za m’ma 1980 akumasulira mabuku a Chizulu pogwiritsa ntchito makina ochita kupukusa

Vuto lalikulu limene linalipo ndi kupeza malo abwino oti omasulira chinenero cha Chizulu azikhala. Ku South Africa kunali lamulo loti anthu akuda ndi azungu asamakhale dera limodzi. Choncho omasulira Chizulu anakakamizika kukakhala nyumba zina kunja kwa Beteli. Zimenezi zinkachititsa kuti abalewa azithera nthawi yambiri kuyenda, ndalama zinkawonongedwa zambiri komanso pankachitika mavuto ena. Mwachitsanzo, pa nthawi ina, anthu 20 omasulira Chizulu ankakhala chipinda chimodzi. M’bale Alfred Phatswana anali mmodzi wa anthu amene anakhala movutikira chonchi kwa zaka ziwiri chakumayambiriro kwa chaka cha 1981. Panopa m’baleyu akutumikira mu Komiti ya Nthambi ya South Africa, ndipo ananena kuti: “Sizinali zophweka kukhala malo oterewa. Komabe tinkasangalala kuti tinali ndi malo okhala omwe anatithandiza kuti tithandize nawo pa ntchito yomasulira. Komanso tinkayesetsa kusamalira malo athuwo kuti azioneka aukhondo nthawi zonse ndipo zimenezi zinathandiza kuti anthu ena azilemekeza Yehova.”

Tikusangalala kwambiri kuti panopa abale ndi alongo athu ku South Africa akugwira ntchito ndi kukhala limodzi mogwirizana ku ofesi ya omasulira mabuku yomwe ili ku Durban, m’dziko la South Africa. Panopa ofalitsa opitirira 28,000 omwe akutumikira m’mipingo ya Chizulu yokwana 584 akupitiriza kusangalala ndi Nsanja ya Olonda komanso mabuku ena ofotokoza Baibulo am’chilankhulo chawo.

Pamwamba: Ofesi yomasulira mabuku ku Durban, South Africa. M’munsi: Abale ndi alongo omwe akutumikira ku ofesiyi. Kumanja: M’bale ndi mlongo akulalikira uthenga wabwino pogwiritsa ntchito Nsanja ya Olonda ya Chizulu

N’zosangalatsa kuti Yehova akupitiriza kudalitsa ntchito yomwe abale ndi alongo omwe amamasulira Nsanja ya Olonda ndiponso mabuku ena m’Chizulu akugwira. Zimenezi zikuthandiza kuti anthu ambiri “amwe madzi opatsa moyo kwaulere”​—Chivumbulutso 22:17.