24 OCTOBER, 2016
TURKMENISTAN
Kodi a Bahram Hemdemov Amasulidwa Nawo Ulendo Ukubwerawu?
M’mwezi wa February 2016, boma la Turkmenistan linamasula akaidi ambiri koma pa nthawiyo silinamasule a Bahram Hemdemov. Patangodutsa miyezi itatu, nkhani ya kumangidwa kwawo inakachitidwa apilo ndipo khoti lalikulu la Turkmenistan linakana kulandira kalata yawo ya apilo. Pa 15 August 2016, loya wa a Hemdemov analembera kalata yodandaula ku Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu.
A Mboni za Yehova Akuzunzidwa ku Turkmenabad
Tsiku limene a Hemdemov ankamangidwa mu March 2015, a Hemdemov ankachititsa msonkhano wamtendere ndi a Mboni anzawo kunyumba kwawo ku Turkemenabad. Apolisi anangobwera popanda chilolezo ndipo analowa m’nyumbayo n’kuyamba kufufuzamo zinthu. Anatenga zinthu zina za a Hemdemov komanso anamenya anthu onse omwe anali m’nyumbayo.
Loya woimira a Hemdemov ananena kuti: “Apolisi anachitira nkhanza a Hemdemov n’cholinga chofuna kuopseza a Mboni ena a ku Turkmenabad.” Ngakhale kuti a Hemdemov anachitiridwa nkhanzazi, anakhalabe okhulupirika.
Akuyembekezera Kuti Atulutsidwa M’ndende
A Mboni za Yehova akuyembekezera kuti posachedwa boma la Turkmenistan litulutsa a Hemdemov m’ndende. Zidzakhala bwino kwambiri ngati ulendo wotsatira akamadzatulutsa anthu kundende, mtsogoleri wa dzikolo a Gurbanguly Berdimuhamedov adzatulutsenso a Hemdemov.
Mkazi wa a Hemdemov dzina lake Gulzira ndi ana awo 4, akuwasowa kwambiri a Hemdemov. Komanso a Mboni anzawo ku Turkmenabad akufunitsitsa kudzawaonanso atabwerako. A Mboni za Yehova m’dziko la Turkmenistan akupempha boma kuti liziwalola kulambira mwamtendere pamodzi ndi anzawo popanda kuopsezedwa ndi akuluakulu a boma.