Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JULY 1, 2019
UKRAINE

A Mboni za Yehova ku Ukraine Anaonetsa Anthu Mabaibulo M’malo Osiyanasiyana

A Mboni za Yehova ku Ukraine Anaonetsa Anthu Mabaibulo M’malo Osiyanasiyana

A Mboni za Yehova ku Ukraine anachita zionetsero zapadera za Baibulo pofuna kudziwitsa anthu za kutulutsidwa kwa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la Chinenero Chamanja cha ku Russia, ndipo kutulutsidwa kwa Baibuloli ndi chinthu chosaiwalika pa ntchito yomasulira yomwe a Mboni za Yehova amagwira. Zionetserozi zinayamba pa 7 October, 2018, mumzinda wa Lviv ndipo zinapitirira mpaka pa 7 June, 2019. Mizinda inanso kumene kunachitikira zionetserozi inali ya Kharkiv, Kyiv, Odesa, ndi Dnipro.

Chionetsero chisanachitike mumzinda uliwonse, mipingo ya chinenero chamanja inkaitanira anthu a vuto losamva a m’madera omwe chionetserocho chikachitikire pogwiritsa ntchito timapepala komanso mavidiyo. Kuonjezera pamenepo, Dipatimenti Yoona Zofalitsa Nkhani ku ofesi ya nthambi ya ku Ukraine inagawira timapepala ndiponso mavidiyo oitanira anthu ku zionetserozi kwa aphunzitsi, ofalitsa nkhani, komanso kwa akuluakulu a boma.

Chionetsero choyamba chinachitikira pa Lviv City Deaf Club, ndipo anthu omwe anabwera anasonyezedwa mapulogalamu osiyanasiyana a pakompyuta ndiponso pazipangizo zamakono omwe anthu a vuto losamva angagwiritse ntchito pophunzira Baibulo, monga pulogalamu ya JW Library Sign Language®. Anthuwo anasangalalanso kuona malo omwe ankasonyeza mmene Baibulo lakhala likuonekera kwa zaka zambiri, kuyambira pamene linali la mipukutu n’kufika pokhala buku monga mmene lilili masiku ano. Mwachitsanzo, anaona Baibulo lomwe linapangidwa mu 1927.

Ndife osangalala kuti Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la Chinenero Chamanja cha ku Russia layamba kupezeka. Tikukhulupirira kuti Baibuloli lithandiza anthu omwe amagwiritsa ntchito Chinenero Chamanja cha ku Russia kuti adziwe Malemba molondola.—Mateyu 5:3.