APRIL 7, 2014
UZBEKISTAN
Kodi Zinthu Ziyamba Kuwayendera Bwino a Mboni za Yehova ku Uzbekistan?
A Mboni za Yehova ku Uzbekistan akukhulupirira kuti akuluakulu a boma awavomereza kuti azilambira Mulungu popanda kuwasokoneza. Bambo Igor Yurchenko, omwe ndi munthu wa Mboni za Yehova amene wakhala akukambirana nkhaniyi ndi akuluakulu a boma la Uzbekistan m’chaka cha 2013, anati: “Zokambirana zathu ndi akuluakulu a bomawa zikuyenda bwino kwambiri, ndipo zikuoneka kuti akusintha maganizo. Tikukhulupirira kuti posachedwapa zinthu ziyamba kutiyendera bwino.”
Umboni wakuti mwina zinthu ziyamba kuyenda bwino ndiwakuti, pa March 2, 2013, akuluakulu a boma la Uzbekistan anatulutsa m’ndende bambo Abdubannob Akhmedov. Bambowa anawatulutsa m’ndende atakhalamo zaka 4 ndi hafu, pa za 6 ndi hafu zimene analamulidwa kuti akhale m’ndende. Iwo anali m’gulu la anthu atatu a Mboni amene anamangidwa chifukwa cholambira Mulungu wawo mwa mtendere. Anzawo ena awiriwo ndi amene anayamba kutulutsidwa m’ndende mu 2012. Pofika pano, palibe munthu wa Mboni amene ali m’ndende ku Uzbekistan.
Patapita miyezi ingapo Bambo Akhmedov atatulutsidwa m’ndende, akuluakulu a boma la Uzbekistan anayamba kuyesetsa kwambiri kuchita zinthu zolemekeza ufulu wachibadwidwe wa anthu. Mwachitsanzo, pa July 5, 2013, boma la Uzbekistan linadziwitsa nthambi ya bungwe la United Nations, Yoona za Ufulu Wachibadwidwe, kuti likuyesetsa kulemekeza ufulu umene anthu ali nawo pa nkhani yolambira Mulungu. Boma la Uzbekistan linafotokoza zimenezi pa msonkhano wa bungweli umene umachitika nthawi ndi nthawi, wounikanso zimene mayiko akuchita pa nkhani yolemekeza ufulu wachibadwidwe.
A Mboni Akuyesetsa Kuti Alembetse Mipingo Yatsopano ku Boma
Panopa, mpingo umodzi wokha wa Mboni za Yehova ndi umene unalembetsedwa ku boma m’dziko la Uzbekistan. Mpingowu uli m’tauni ya Chirchik m’dera la Tashkent. Komabe anthu ambiri a Mboni za Yehova amakhala m’madera osiyanasiyana m’dzikoli. Kuyambira m’chaka cha 1996, zakhala zovuta kuti a Mboniwa alembetse mipingo yawo yatsopano ku boma. Ngakhale kuti amasonkhana kuti azilambira Mulungu wawo mwamtendere, amachita zinthu mwamantha chifukwa palibe lamulo limene lingawateteze ndipo akhoza kuimbidwa mlandu. Bambo Yurchenko anapitiriza kunena kuti: “Tikukhulupirira kuti zokambirana zathu ndi akuluakulu a boma zichititsa kuti zinthu ziyambe kutiyendera bwino. Zithandizanso kuti tilembetse ku boma mipingo yonse ya Mboni za m’dziko lino la Uzbekistan.”
A Mboni za Yehova akuyembekezera zoti ayamba kulambira Mulungu wawo mwamtendere m’dziko la Uzbekistan. Iwo akukhulupiriranso kuti posachedwapa, akuluakulu a boma akhoza kuvomereza kuti alembetse mipingo yawo yatsopano.