Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

FEBRUARY 24, 2020
ZATSOPANO

Gawo Latsopano—Kufotokoza Mavesi a M’Baibulo

Gawo Latsopano—Kufotokoza Mavesi a M’Baibulo

Webusaiti ya jw.org tsopano ili ndi gawo lakuti, “Kufotokoza Mavesi a M’Baibulo.”

Mwezi uliwonse anthu ambiri amafufuza pa intaneti kuti adziwe zimene mavesi osiyanasiyana a m’Baibulo amatanthauza. Pofuna kuthandiza anthuwa, gawo lakuti “Kufotokoza Mavesi a M’Baibulo” lizikhala ndi matanthauzo komanso mfundo zofotokoza mavesi osiyanasiyana.

Onani gawo lakuti, “Kufotokoza Mavesi a M’Baibulo” pawebusaiti yathu pansi pa mawu akuti, “Zimene Baibulo Limaphunzitsa” ndiponso pa pulogalamu ya JW Library pansi pa mawu akuti “Article Series.”