Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndingatani Ngati Bambo Kapena Mayi Anga Atayamba Kudwala?

Kodi Ndingatani Ngati Bambo Kapena Mayi Anga Atayamba Kudwala?

 Munthu akakhala mwana, amaona kuti si udindo wake kusamalira munthu wina amene akudwala. Zimenezi zimachitika kwambiri chifukwa nthawi imeneyi makolo ake amakhala adakali amphamvu.

 Koma kodi mungatani ngati bambo kapena mayi anu atayamba kudwala inuyo mudakali wamng’ono? Tiyeni tikambirane za atsikana awiri omwe anakumana ndi vuto limeneli.

 Emmaline

 Mayi anga ali ndi matenda a Ehlers-Danlos. Matendawa amatenga nthawi yaitali ndipo amakhudza khungu, mitsempha ya magazi komanso m’malo olumikizana mafupa.

 Matendawa alibe mankhwala ndipo pa zaka 10 zapitazi, mayi anga akhala akuvutika kwambiri ndi matendawa kuposa zaka zonse za m’mbuyomu. Nthawi zina magazi awo ankachepa kwambiri moti moyo wawo unkakhala pa ngozi. Komanso nthawi zina ankamva ululu kwambiri moti ankalakalaka atangofa.

 Tonse m’banja lathu ndife a Mboni za Yehova ndipo anthu a kumpingo wathu akhala akutilimbikitsa kwambiri. Mwachitsanzo, chaposachedwapa mtsikana wina wa msinkhu ngati wanga, anatitumizira khadi lotiuza kuti amatikonda ndiponso kuti ndi wokonzeka kutithandiza. N’zosangalatsa kwambiri kukhala ndi mnzako wa choncho.

 Baibulo landithandizanso kwambiri. Mwachitsanzo, malemba amene amandigwira mtima ndi Salimo 34:18 lomwe limati: “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka.” Komanso la Aheberi 13:6 lomwe limati: “Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa.”

 Makamaka lemba la Aheberi limandilimbikitsa kwabasi. Ndimachita mantha ndikaganizira kuti tsiku lina mayi anga adzamwalira. Ndimawakonda kwambiri ndipo tsiku lililonse tikaonana, ndimathokoza Yehova. Ngakhale sitidziwa za mawa, lembali limandithandiza kuti ndisamachite mantha ndikamaganizira zam’tsogolo.

 Koma palinso chinthu china chomwe chimandichititsa mantha. Matenda a mayi angawa ndi akumtundu. Iwo anawatenga kwa mayi awo, ndipo inenso ndinatengera matendawa kwa mayi angawo. Lemba la Aheberi 13:6, limandilimbikitsa kudziwa kuti Yehova adzakhala “mthandizi wanga” ndikadzayamba kuvutika ndi matendawa.

 Komabe ndimayamikira mwayi womwe ndili nawo panopa ndipo sindiganizira kwambiri zinthu zam’mbuyo kapenanso zam’tsogolo. Ngati nditamangokhalira kuyerekeza zimene mayi anga ankakwanitsa kuchita ndi zimene akulephera kuchita panopa, ndikhoza kumangovutika maganizo. Baibulo limanena kuti mayesero omwe tikukumana nawo nthawi ino, “ndi akanthawi” tikayerekeza ndi moyo wopanda matenda womwe tikuyembekezera.​—2 Akorinto 4:17; Chivumbulutso 21:1-4.

 Zoti muganizire: Kodi N’chiyani chimathandiza Emmaline kuti akhalebe wolimba mtima? Nanga inuyo mungatani kuti mukhalebe wolimba mtima ngati mutakumana ndi mayesero?

 Emily

 Nthawi imene ndinali ku sekondale, bambo anga anayamba kudwala matenda ovutika maganizo. Zinangokhala ngati asintha n’kukhala munthu wina. Kuchokera nthawi imeneyo, bambo amangokhala okhumudwa, amangoopa zilizonse komanso nthawi zambiri amakhala ndi nkhawa kuti zinazake zoopsa zikhoza kuwachitikira. Tsopano patha zaka 15 akulimbana ndi vuto limeneli. Ziyenera kuti zimawapweteka kwambiri akamakhala okhumudwa ngakhale amadziwa kuti safunika kumaganizira zimenezo.

 Banja lathu ndi la Mboni za Yehova ndipo abale ndi alongo akhala akutithandiza kwambiri. Abale ndi alongowa amatikomera mtima komanso amatimvetsa. Palibe aliyense amene anapangitsapo bambo anga kudzimva ngati munthu wosafunika kumpingo. Ndimawakonda kwambiri bambo anga chifukwa ndimaona kuti akuyesetsa kwambiri kupirira matendawa.

 Ndimalakalaka kale likanati lizibwerera, pamene bambo anali munthu wosangalala komanso wopanda nkhawa. Ndimamva chisoni kwambiri ndikamawaona akuvutika ndi matenda tsiku lililonse.

 Komabe, bambo anga amachita zinthu mwakhama kuti asamangoganizira za matenda awo. Nthawi ina atavutika kwambiri ndi matendawa, ankayesetsa kumawerenga Baibulo tsiku lililonse ngakhale kuti ankawerenga mavesi ochepa chabe. Zimenezi zinawathandiza kukhala olimba. Ngakhale kuti zimene ankachitazi zinkaoneka ngati zochepa, koma zinapulumutsa moyo wawo. Nthawi imeneyo ndinasangalala kwambiri ndi zimene ankachita.

 Lemba la Nehemiya 8:10 limandilimbikitsa kwambiri. Lembali limati: “Chimwemwe chimene Yehova amapereka ndicho malo anu achitetezo.” Mfundo imeneyi ndi yoona. Ndimakhala ndi chimwemwe chachikulu ndikakhala kumisonkhano yampingo komanso ndikamapereka ndemanga. Zimenezi zimandithandiza kupeza mphamvu ndikakhala wofooka komanso ndimakhala wosangalala tsiku lonselo. Chitsanzo cha bambo anga chimandithandiza kudziwa kuti kaya tikulimbana ndi vuto lotani, Yehova ndi wokonzeka kutithandiza.

 Zoti muganizire: Kodi Emily amawathandiza bwanji bambo ake? Kodi mungathandize bwanji munthu amene ali ndi matenda ovutika maganizo?