ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA
Kodi Kugonana M’kamwa Kumakhaladi Kugonana?
Bungwe lina la ku United States linachita kafukufuku n’kupeza kuti pa achinyamata azaka pakati pa 15 ndi 19 omwe anawafunsa, pafupifupi hafu anali atagonanapo m’kamwa. Munthu wina amene analemba buku lokhudza kugonana m’kamwa dzina lake Sharlene Azam anati: “Mukafunsa achinyamata za [kugonana m’kamwa] amanena kuti si nkhani yaikulu. Iwo amaona kuti si kugonana kwenikweni.”
Kodi inuyo mukuganiza bwanji?
Yankhani mafunso otsatirawa kuti inde kapena ayi.
Kodi mtsikana angatenge mimba chifukwa chogonana m’kamwa?
Inde
Ayi
Kodi kugonana m’kamwa kungayambitse matenda?
Inde
Ayi
Kodi kugonana m’kamwa kumakhaladi kugonana?
Inde
Ayi
Kodi zoona zake n’zotani?
Yerekezerani mayankho anu ndi amene ali m’munsiwa.
Kodi mtsikana angatenge mimba chifukwa chogonana m’kamwa?
Yankho: Ayi. N’chifukwa chake anthu ambiri amaganiza molakwika kuti kugonana m’kamwa sikungabweretse mavuto.
Kodi kugonana m’kamwa kungayambitse matenda?
Yankho: Inde. Anthu amene amagonana m’kamwa angayambe kudwala matenda a chiwindi (hepatitis A kapena B), njerewere za kumaliseche, chinzonono, mabomu, edzi ndi chindoko.
Kodi kugonana m’kamwa kumakhaladi kugonana?
Yankho: Inde. Kugonana kumaphatikizapo kugonana m’kamwa, kugonana kumatako komanso kuseweretsa maliseche a munthu wina.
Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji?
Ganizirani malemba ena m’Baibulo amene amakhudza nkhani ya kugonana m’kamwa.
Baibulo limati: ‘Mulungu akufuna kuti mupewe dama.’—1 Atesalonika 4:3.
Mawu oyambirira amene anawamasulira kuti “dama,” akutanthauza kugonana, kugonana m’kamwa, kugonana kumatako kapena kuseweretsa maliseche a munthu wina ndipo akutanthauza kuchita zinthuzi ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi wanu. Munthu amene amachita dama angakumane ndi mavuto ambiri. Koma vuto lalikulu n’lakuti akhoza kuwononga ubwenzi wake ndi Mulungu.—1 Petulo 3:12.
Baibulo limati: “Amene amachita dama amachimwira thupi lake.”—1 Akorinto 6:18.
Munthu akhoza kudwala, kuwononga ubwenzi wake ndi Yehova komanso kusokonezeka maganizo chifukwa chogonana m’kamwa. Buku lina limati: “Munthu akagonana ndi munthu wina amene sayenera kugonana naye akhoza kudandaula ndiponso kunong’oneza bondo pambuyo pake. Izi zimakhala choncho ngakhale kuti munthuyo wagonana m’njira ina monga m’kamwa. Mtundu uliwonse wa kugonana ndi kugonana basi.”—Talking Sex With Your Kids.
Baibulo limati: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino.”—Yesaya 48:17.
Kodi mumakhulupirira kuti malamulo a Mulungu okhudza kugonana ndi othandizadi? Kapena kodi mumaona kuti malamulowo ndi ovuta? Kuti muyankhe mafunsowa, ganizirani za msewu waukulu umene mumadutsa magalimoto ambiri. Pamsewuwu pamakhala zikwangwani zokuuzani liwiro limene muyenera kuyenda kapena pamene muyenera kuima. Pamakhalanso maloboti okuuzani pamene muyenera kuima kapena kupita. Kodi mumaona kuti zinthuzi zimakutetezani kapena zimakuletsani kuchita zimene mukufuna? Nanga n’chiyani chingachitike ngati inuyo kapena anthu ena atangozinyalanyaza?
N’chimodzichimodzi ndi malamulo a Mulungu. Mukangowanyalanyaza mumakolola zimene mwafesa. (Agalatiya 6:7) Buku lina limati: “Mukamachita zinthu zotsutsana ndi zimene mumakhulupirira kapena zimene mumadziwa kuti ndi zoyenera, mumayamba kudzimva kuti ndinu opanda pake.” (Sex Smart) Koma munthu amene amatsatira mfundo za Mulungu, sadziimba mlandu ndipo anthu ena amamulemekeza.—1 Petulo 3:16.