Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kukhala Pachibwenzi​—Mbali Yoyamba: Kodi Ndine Wokonzeka Kukhala Pachibwenzi?

Kukhala Pachibwenzi​—Mbali Yoyamba: Kodi Ndine Wokonzeka Kukhala Pachibwenzi?

 Kodi kukhala pachibwenzi n’kutani?

 Anthu ena amakhala pachibwenzi ndi cholinga chongosangalala basi. Munkhaniyi, mawu akuti “kukhala pachibwenzi” akutanthauza nthawi imene mwamuna ndi mkazi amacheza limodzi ndi cholinga chofuna kudziwa ngati ali oyenererana kudzakwatirana kapena ayi. Choncho anthu omwe ali pachibwenzi amafunika kukhala ndi cholinga. Koma cholinga cha chibwenzi si kungosangalala kucheza ndi mwamuna kapena mkazi basi.

 M’kupita kwa nthawi, anthu amene ali pachibwenzi akhoza kusankha kukwatirana kapena ayi. Mukakhala pachibwenzi muyenera kukonzekera chilichonse chomwe chingachitike.

 Mfundo yofunika kwambiri: Ngati mukuona kuti ndinu wokonzeka kukhala pachibwenzi, ndiye kuti ndinunso okonzeka kukhala pabanja.

Kukhala pachibwenzi ulibe cholinga cholowa m’banja, kuli ngati kupita kumayeso a ntchito ulibe cholinga choyamba ntchitoyo

 Kodi mwakonzeka kukhala pachibwenzi?

 Ngati muli pachibwenzi, muzidziwa kuti mukhoza kudzalowa m’banja, choncho ndi bwino kuganizira makhalidwe anu omwe angathandize kapena kusokoneza mgwirizano wanu. Mwachitsanzo, ganizirani izi:

  •   Zomwe mumachita ndi anthu am’banja lanu. Mmene mumachitira zinthu ndi makolo komanso achibale anu makamaka pamene muli ndi nkhawa, nthawi zambiri zimasonyeza mmene muzidzachitiranso zinthu ndi mwamuna kapena mkazi wanu.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Kuwawidwa mtima konse kwa njiru, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu achipongwe zichotsedwe mwa inu limodzi ndi zoipa zonse.”​—Aefeso 4:31.

     Dzifunseni kuti: ‘Kodi makolo ndi achibale anga anganene kuti ndimachita nawo zinthu mwaulemu? Ndikasemphana maganizo ndi munthu wa m’banja langa, kodi ndimakambirana nawo modekha, kapena ndimapsa mtima n’kukangana nawo?’

    Ngati panopa mumalephera kuthetsa kusamvana ndi makolo anu, kodi mungadzakwanitse kuchita zimenezo ndi mwamuna kapena mkazi wanu?

  •   Kudzimana zinthu zina. Ukakhala m’banja, umafunika kuganizira zimene mnzako akufuna ndi zimene sakufuna ndipo nthawi zambiri pamafunika kulolerana

     Mfundo ya m’Baibulo: “Aliyense asamangodzifunira zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina.”​—1 Akorinto 10:24.

     Dzifunseni kuti: ‘Kodi nthawi zonse ndimakakamira maganizo anga? Kapena ndimamvanso maganizo a ena? Kodi ndimatani pa nkhani yoganizira zofuna za ena kuposa zanga?’

  •   Kudzichepetsa. Mwamuna kapena mkazi wabwino amavomereza akalakwitsa komanso amapepesa kuchokera pansi pa mtima.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Paja tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.”​—Yakobo 3:2.

     Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimakhala wokonzeka ndikalakwitsa, kapena ndimapereka zifukwa zodzikhululukira? Kodi ndimakhumudwa kwambiri anthu ena akandipatsa malangizo okhudza zinthu zimene ndikufunika kusintha?’

  •   Ndalama. Nkhani zokhudza ndalama ndi zimene zimayambitsa mavuto ambiri m’banja. Koma ngati mumatha kugwiritsa ntchito bwino ndalama, simungavutike kuthetsa kusamvana pa nkhani zoterezi.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja sayamba wakhala pansi ndi kuwerengera ndalama zimene adzawononge, kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kumalizira nsanjayo?”​—Luka 14:28.

     Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimadziletsa pa nkhani za ndalama, kapena ndimangokhalira ngongole? Kodi ndachita zotani m’mbuyomu zosonyeza kuti ndimagwiritsa ntchito bwino ndalama?’

  •   Moyo wauzimu. Ngati ndinu wa Mboni za Yehova, muyenera kukhala ndi pulogalamu yokhazikika yophunzira Baibulo komanso kupezeka pamisonkhano ya Chikhristu.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”​—Mateyu 5:3.

     Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimayesetsa kuchita zinthu zothandiza kuti chikhulupiriro changa chikhale cholimba? Kodi ndimaona kuti pulogalamu yanga yauzimu ndi yofunika kwambiri, kapena ndimalola zinthu zina kundisokoneza?’

 Mfundo yofunika kwambiri: Anthufe timafunikira munthu wa makhalidwe abwino womanga naye banja. Ngati mukuyesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino, n’zosavuta kuti munthu winanso wa makhalidwe abwino akopeke nanu.