Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa?—Gawo 4: Kodi Ndingafotokozere Bwanji Munthu Kuti Zinthu Zinachita Kulengedwa?

Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa?—Gawo 4: Kodi Ndingafotokozere Bwanji Munthu Kuti Zinthu Zinachita Kulengedwa?

Mumakhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa koma zimakuvutani kunena zimenezi kusukulu. Mwina zili choncho chifukwa kusukulu mumaphunzira kuti zinthu zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Ndiye mukuona kuti aphunzitsi komanso anzanu akusekani mukanena kuti zinthu zinachita kulengedwa. Kodi mungatani kuti muzifotokoza molimba mtima?

 Musamadziderere

 Mwina mungaganize kuti: ‘Sayansi imandivuta ndiye sindingathe kufotokozera munthu umboni woti zinthu zinachita kulengedwa.’ Mtsikana wina dzina lake Danielle nthawi ina analinso ndi maganizo amenewa. Iye ananena kuti: “Ndinkadana ndi zoti ndizitsutsana ndi aphunzitsi komanso anzanga.” Mtsikana winanso dzina lake Diana ananena kuti: “Ndinkabalalika kwambiri akamanditsutsa pogwiritsa ntchito mawu ozama a sayansi.”

 Komatu cholinga chanu si kufuna kusonyeza kuti inuyo ndiye wodziwa. Ndipo ubwino wina ndi wakuti simukufunika kuchita kukhala wodziwa kwambiri sayansi kuti muthe kufotokozera munthu umboni wosonyeza kuti n’zomveka kukhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa.

 Zimene zingakuthandizeni: Mukhoza kugwiritsa ntchito umboni wosavuta kumva umene uli m’Baibulo palemba la Aheberi 3:4: “Nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.”

 Mtsikana wina wazaka 24 dzina lake Carol amagwiritsa ntchito lemba la Aheberi 3:4 pofotokozera munthu. Iye amanena kuti: “Tiyerekeze kuti mukuyenda m’nkhalango yowirira kwambiri ndipo simukuona chilichonse chosonyeza kuti m’nkhalangoyi mungakhale munthu. Ndiyeno mutayang’ana pansi mukuona kamtengo kamachesi. Kodi mungaganize kuti kanapezekapo bwanji? Anthu ambiri angaganize kuti, ‘Munthu winawake ayenera kuti anadutsapo kuno.’ Ndiye ngati kamtengo kamachesi kakang’ono ngati kameneko kakusonyeza umboni woti m’nkhalangomo munadutsapo munthu, ndiye kuli bwanji chilengedwe chonsechi komanso zinthu zonse zimene zilimozi?”

 Ngati munthu atakufunsani kuti: “Ngati zili zoona kuti zinthu zinachita kulengedwa, ndiye ndi ndani analenga Mlengi?”

 Mungayankhe kuti: “Kulephera kumvetsa zinthu zonse zokhudza Mlengi si umboni woti iyeyo kulibeko. Mwachitsanzo, zikhoza kutheka kuti simudziwa zonse zokhudza munthu amene anapanga foni yanu ya m’manja. Komabe mumakhulupirira kuti pali winawake amene anaipanga. Si choncho? [Yembekezerani ayankhe.] Pali zinthu zambiri zimene tingadziwe zokhudza Mlengi. Ngati mungakonde, ndikhoza kukufotokozerani zimene ndaphunzira zokhudza Mlengi.”

 Muzikhala wokonzeka

 Baibulo limanena kuti muzikhala “okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho, koma ayankheni ndi mtima wofatsa ndiponso mwaulemu kwambiri.” (1 Petulo 3:15) Choncho muziganizira zinthu ziwiri zofunika izi: (1) Zimene munganene. (2) Mmene mungazinenere.

  1.   Zimene munganene. Kukonda Mulungu ndi kumene kungakulimbikitseni kuti munene zoti zinthu zinachita kulengedwa. Komabe kungouza anthu kuti mumakonda Mulungu sikungakhale kokwanira kuti aone umboni wosonyeza kuti zinthu zonse zinalengedwa ndi Mulungu. Mungachite bwino kugwiritsa ntchito zitsanzo za m’chilengedwechi posonyeza umboni woti n’zomveka kukhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa.

  2.   Mmene mungazinenere. Muzinena motsimikiza koma osati mwamwano kapena mosonyeza kuti ndinu wodziwa kwambiri. Anthu angamvetsere zimene mukunena ngati mukusonyeza kuti mumalemekeza zimene amakhulupirira komanso ufulu wawo wosankha zimene akufuna kutsatira.

     “Ndikuona kuti ndi bwino kupewa kulankhula monyoza kapena mosonyeza ngati iweyo umadziwa zambiri kuposa iwowo. Anthu sangamvetsere ngati mawu athu akumveka mosonyeza kuti ifeyo ndiye odziwa zinthu.”​—Elaine.

 Zimene mungagwiritse ntchito

Kukonzekera mmene mungafotokozere zimene mumakhulupirira kuli ngati kukonzekera zimene mungavale nyengo ikasintha

 Mtsikana wina dzina lake Alicia ananena kuti “Ngati munthu sunakonzekere zoti unene, umangokhala osanena chilichonse poopa kuchita manyazi.” Zimene Alicia ananenazi zikusonyeza kuti zinthu zimayenda bwino munthu ukakonzekera. Mtsikana winanso dzina lake Jenna ananena kuti: “Sindivutika kufotokozera munthu kuti zinthu zinachita kulengedwa ndikakonzekera chitsanzo chachidule chosonyeza umboni wa zimene ndikumuuzazo.”

 Kodi mungapeze kuti zitsanzo? Achinyamata ambiri zinthu zinawayendera bwino chifukwa chogwiritsa ntchito zinthu zotsatirazi:

 Mungaonenso nkhani zakuti, “Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa?” zomwe zinatuluka m’mbuyomu.

  1.  Gawo 1: N’chifukwa Chiyani Ndimakhulupirira Kuti Kuli Mulungu?

  2.  Gawo 2: N’chifukwa Chiyani Simuyenera Kungokhulupirira Zoti Zinthu Zinangokhalako Zokha?

  3.  Gawo 3: N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kukhulupirira Kuti Zinthu Zinachita Kulengedwa?

 Zimene zingakuthandizeni: Pezani zitsanzo zomwe mumaziona kuti n’zomveka. Zitsanzo zotere zingakuthandizeni kuti musaziiwale komanso kuti muzifotokoze motsimikiza. Kenako yesererani mmene mungafotokozere zimene mumakhulupirira.