ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA
Kodi Ndingatani Ngati Ndili ndi Matenda Ovutika Maganizo?
Kutsatira njira zabwino polimbana ndi vutolo kungakuthandizeni kuti muyambe kumva bwino.
Kodi mungatani?
Taganizirani zochitika izi:
Jennifer sakusangalalanso. Tsiku lililonse amangokhalira kulira pachifukwa chosadziwika bwino. Safuna kucheza ndi anthu komanso kudya. Iye amavutika kugona kapena kuchita zinthu zina. Iye akudzifunsa kuti: ‘Kodi chikundichitikira n’chiyani? Koma ndidzakhalanso bwinobwino?’
Mark anali mwana wabwino kusukulu. Koma tsopano wayamba kudana ndi sukulu ndipo sakukhozanso bwino ngati kale. Iye alibenso mphamvu zochitira masewera amene kale ankawakonda kwambiri. Azinzake sakumvetsa. Makolo ake akudandaula. Kodi zimene zikumuchitikirazi ndi zimene zimachitira aliyense akamakula kapena pali chinachake?
Kodi nthawi zambiri nanunso mumamva ngati Jennifer kapena Mark? Ngati ndi choncho, kodi mungatani? Mukhoza kuyesa kuchita zinthu ziwirizi:
Kulimbana ndi vutolo panokha
Kufotokozera munthu wina wamkulu yemwe mumamudalira.
Njira A ingaoneke ngati yabwino makamaka ngati simukufuna kuuza aliyense. Koma kodi ndi njira yabwino? Baibulo limati: “Awiri amaposa mmodzi,. . . Ngati mmodzi wa iwo atagwa, winayo akhoza kum’dzutsa mnzakeyo. Koma kodi zingakhale bwanji munthu mmodzi atagwa popanda wina woti am’dzutse?”—Mlaliki 4:9, 10.
Mwachitsanzo: Tiyerekeze kuti mwasochera ndipo muli kumalo ena ake amene kumakonda kuchitika za uchifwamba. Kunja kwada ndipo mukuona anthu osawadziwa abisala m’malo osiyanasiyana. Kodi mungachite chiyani? Mungathe kufufuza nokha njira yoti muchokere ku malo oopsawo. Koma kodi sichingakhale chinthu chanzeru kupempha munthu wina wodalirika kuti akuthandizeni?
Kuvutika maganizo kuli ngati malo oopsa amenewa. N’zoona kuti nthawi zina mungamavutike maganizo kwa kanthawi kochepa. Koma ngati kuvutika maganizo kukupitirira kwa nthawi yayitali, mungachite bwino kupempha munthu wina kuti akuthandizeni.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Wodzipatula . . . amachita zosemphana ndi nzeru zonse zopindulitsa.”—Miyambo 18:1.
Ubwino wogwiritsa ntchito njira B, yomwe ndi kufotokozera makolo anu kapena munthu wina wamkulu yemwe mumamudalira, ndi woti mukhoza kupindula ndi zimene zinathandiza munthu wina amene analimbana ndi kuvutika maganizo.
Mwina munganene kuti: ‘Makolo anga sangamvetse mmene ndikumvera.’ Koma kodi muli ndi umboni woti sangakumvetsenidi? Ngakhale kuti mavuto amene anakumana nawo ali ana angakhale osiyana ndi amene inuyo mukukumana nawo, n’kutheka kuti ankamva ngati mmene inuyo mukumvera. Makolo anu akhoza kudziwa njira yothetsera vuto lanulo.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Kodi okalamba si paja amakhala ndi nzeru, Ndipo amene akhala masiku ambiri si paja amamvetsa zinthu?”—Yobu 12:12.
Mfundo yake: Ngati mungafotokozere makolo anu kapena munthu wina wamkulu wodalirika, n’zosakayikitsa kuti angakupatseni malangizo amene angakuthandizeni.
Bwanji ngati ndi vuto lofunika azachipatala?
Ngati mumavutika maganizo tsiku lililonse, mukhoza kukhala kuti muli ndi matenda ovutika maganizo omwe angafunike kuti azachipatala akuthandizeni.
Kwa achinyamata, zizindikiro za matenda ovutika maganizo zingafanane ndi zimene zimachitikira mwana akamasintha n’kukhala wachinyamata. Nthawi zina amasangalala nthawi zina sasangalala, koma zizindikirozo za munthu wovutika maganizo zimakhala zamphamvu kwambiri komanso zimachitika kwa nthawi yayitali. Choncho ngati mumakhala wokhumudwa kwambiri komanso kwa nthawi yayitali, mungachite bwino kuuza makolo anu kuti mupite kuchipatala.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Anthu abwinobwino safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.”—Mateyu 9:12.
Ngati mutapezeka kuti muli ndi matenda ovutika maganizo, palibe chifukwa chochitira manyazi ndi zimenezi. Achinyamata ambiri amakhala ndi vuto lovutika maganizo koma n’zotheka kulithetsa. Anzanu omwe amakukondani sangakunyozeni chifukwa cha vuto lanulo.
Zimene zingakuthandizeni: Khalani woleza mtima. Zimatenga nthawi kuti munthu achire matenda ovutika maganizo ndipo muyenera kuyembekezera kuti masiku ena muzisangalala pomwe ena ayi. a
Zimene zingakuthandizeni kuti muchire
Ngakhale kuti vuto lanu lingafunike azachipatala, pali zinthu zina zomwe inuyo mungachite ngati mukuvutika maganizo kwa nthawi yayitali. Mwachitsanzo, kuchita masewera olimbitsa thupi, kudya chakudya chopatsa thanzi komanso kugona mokwanira, zingakuthandizeni kuti maganizo anu akhazikike. (Mlaliki 4:6; 1 Timoteyo 4:8) Mungachitenso bwino mutakhala ndi buku lolembamo mmene mukumvera, zimene mungachite kuti muchire, zimene zingakubwezereni m’mbuyo, komanso zimene mukuchita bwino.
Kaya mukudwala matenda ovutika maganizo kapena mukungokumana ndi zinthu zimene zikukusokonezani, kumbukirani kuti: Ngati mungalole kuti anthu ena akuthandizeni komanso kuchita zinthu zina zomwe zingakuthandizeni kuti muchire, mukhoza kulimbana ndi vuto lovutika maganizo.
Malemba a m’Baibulo amene angakuthandizeni
“Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”—Salimo 34:18.
“Umutulire Yehova nkhawa zako, Ndipo iye adzakuchirikiza. Sadzalola kuti wolungama agwedezeke.”—Salimo 55:22.
“Ine, Yehova Mulungu wako, ndagwira dzanja lako lamanja. Ine amene ndikukuuza kuti, ‘Usachite mantha. Ineyo ndikuthandiza.”—Yesaya 41:13.
“Musamade nkhawa za tsiku lotsatira.”—Mateyu 6:34.
“Zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu.”—Afilipi 4:6, 7.
a Ngati mwayamba kukhala ndi maganizo ofuna kudzipha, pemphani munthu wamkulu wodalirika kuti akuthandizeni mwamsanga. Kuti mudziwa zambiri, onani nkhani yokhala ndi mbali 4 ya mutu wakuti “Kodi Kudzipha Ndi Njira Yothetsera Mavuto?” mu Galamukani! ya April 2014.