Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndingasankhe Bwanji Munthu Wabwino Woti Ndizimutsanzira?

Kodi Ndingasankhe Bwanji Munthu Wabwino Woti Ndizimutsanzira?

 “Ndikakumana ndi mavuto enaake ku sukulu, ndinkangoganizira munthu amene ndinkasirira makhalidwe ake yemwenso anakumana ndi mavuto ofanana ndi angawo. Kenako ndimayesetsa kutengera chitsanzo chake. Kukhala ndi munthu winawake woti ndizimutsanzira kunandithandiza kwambiri pa nthawi imene ndinkakumana ndi mavuto.”​—Haley.

 Kukhala ndi munthu woti muzimutsanzira kungakuthandizeni kupewa mavuto komanso kukwaniritsa zolinga zanu. Koma chinsinsi chagona pa kusankha munthu wabwino.

 N’chifukwa chiyani muyenera kusankha mwanzeru?

  •   Munthu yemwe mungasankhe kuti muzimutsanzira angakuchititseni kuti muzichita zabwino kapena zoipa.

     Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti aziona zochita za anthu azitsanzo zabwino ndipo limati: “Ndipo pamene mukuonetsetsa zotsatira zabwino za khalidwe lawo, tsanzirani chikhulupiriro chawo.”​—Aheberi 13:7.

     Zimene Zingakuthandizeni: Popeza kuti anthu omwe mungasankhe angachititse kuti muzichita zabwino kapena zoipa, muziyesetsa kusankha anthu omwe ali ndi makhalidwe abwinodi osati kungosankha anthu otchuka kapenanso a zaka zofanana ndi zanu.

     “Ndinaphunzira zambiri kwa Adam yemwe ndi Mkhristu mnzanga. Iye ali ndi maganizo abwino komanso khalidwe labwino. Mpaka pano ndimakumbukirabe zinthu zina zomwe ankanena ndi kuchita. Komatu iyeyo sadziwa kuti khalidwe lake linandithandiza kwambiri.”​—Colin.

  •   Zochita za anthu omwe mungasankhe kuti muziwatsanzira zingakhudze mmene mumaganizira komanso mmene mumamvera.

     Baibulo limati: “Musasocheretsedwe. Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.”​—1 Akorinto 15:33.

     Zimene Zingakuthandizeni: Sankhani munthu yemwe alidi ndi makhalidwe abwino osati yemwe amangooneka ngati wa khalidwe labwino. Mukangotengera mmene munthu akuonekera mutha kukhumudwa pamapeto pake.

     “Ukamadziyerekezera ndi anthu ooneka bwino umadziona kuti ndiwe wosafunika komanso wachabechabe. Zimenezi zingakuchititse kuti uzingoganizira mmene iweyo umaonekera.”​—Tamara.

     Zoti muganizire: Kodi pangakhale mavuto otani ngati mungasankhe anthu otchuka kapena opanga masewera enaake kuti ndi amene muziwatsanzira?

  •   Anthu omwe mungasankhe angachititse kuti mukwaniritse zolinga zanu kapena ayi.

     Baibulo limati: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.”​—Miyambo 13:20.

     Zimene Zingakuthandizeni: Muzisankha anthu a makhalidwe abwino omwe inuyo mumafuna mutakhala nawo. Ndipo mukamaona zochita zawo mutha kuzindikira zimene nanunso mungachite kuti mukwanitse kukhala ndi makhalidwewo.

     “M’malo mongonena kuti ‘Ndikufuna nditakhala munthu wodalirika,’ ndi bwino kunena kuti, ‘Ndikufuna nditakhala munthu wodalirika ngati Jane. Iye amasunga nthawi ndipo ndi wakhama pochita zinthu.’”​—Miriam.

     Mfundo yofunika kwambiri: Mukasankha munthu wabwino woti muzimutsanzira zimakuthandizani kuti nanunso mudzakhale munthu wabwino.

Sungavutike kukwaniritsa zolinga zako zabwino ngati wasankha anthu abwino oti uziwatsanzira.

 Kodi mungasankhe bwanji?

 Pali njira ziwiri zomwe mungagwiritse ntchito posankha munthu womutsanzira.

  1.   Mungasankhe khalidwe linalake lomwe mumafuna mutakhala nalo, kenako pezani munthu amene mumasirira yemwe ali ndi khalidwelo.

  2.   Mungasankhe munthu yemwe mumamusirira kenako mungasankhe khalidwe labwino linalake lomwe ali nalo limene mukufuna mutakhala nalo.

 Gawo la zoti muchite lomwe lili m’nkhani ino lingakuthandizeni kuchita zimenezi.

 Anthu omwe mungawatsanzire angakhale:

  •  Achinyamata anzanu: “Ndinasankha munthu yemwe ndikufuna kutengera makhalidwe ake kuti akhale mnzanga wapamtima. Iye amapeza nthawi yosamalira anthu ena. Ndi wamng’ono kwa ine koma ali ndi makhalidwe abwino amene ineyo ndilibe, ndipo zimenezi zimandichititsa kuti ndiyesetse kumutsanzira.”​—Miriam.

  •  Akuluakulu. Angakhale makolo anu kapenanso Akhristu anzanu. “Kunena zoona makolo anga ndi zitsanzo zabwino. Ali ndi makhalidwe abwino. Ngakhale kuti ndimaona zolakwa zawo, koma ndimadziwanso kuti ndi okhulupirika. Ndikukhulupirira kuti nanenso ndikadzakhala ndi ana nawonso adzaona kuti ndine chitsanzo chawo chabwino.”​—Annette.

  •  Anthu otchulidwa m’Baibulo. Ndinasankha anthu amakhalidwe abwino angapo kuchokera m’Baibulo monga Timoteyo, Rute, Yobu, Petulo ndi kamtsikana ka Chiisiraeli pa zifukwa zosiyanasiyana. Ndikamaphunzira zambiri zokhudza anthu otchulidwa m’Baibulo m’pamene ndimaona kuti ndi enieni. Kuphunzira nkhani za m’buku lakuti Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo, kwandithandiza kwambiri. Komanso gawo lakuti ‘Zitsanzo Zabwino’ lomwe lili m’mabuku akuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa landithandizanso kwambiri.”​—Melinda.

 Zimene Zingakuthandizeni: Musangokhala ndi munthu mmodzi yemwe mukufuna kumutsanzira. Mtumwi Paulo anauza Akhristu anzake kuti: “Muzionetsetsa amene akuyenda mogwirizana ndi chitsanzo chimene tinakupatsani.”—Afilipi 3:17.

 Kodi mukudziwa? Inunso mukhoza kukhala chitsanzo chabwino cha munthu wina. Baibulo limati: “Ukhale chitsanzo kwa okhulupirika m’kalankhulidwe, m’makhalidwe, m’chikondi, m’chikhulupiriro, ndi pa khalidwe loyera.”—1 Timoteyo 4:12.

 “Ngakhale kuti nanu mumafunika kusintha zinthu zina koma mukhozabe kuthandiza ena kutengera makhalidwe anu abwino. Simungadziwe kuti ndi anthu angati amene amaona makhalidwe anuwo ndiponso kuti zimene mungayankhule zingathandize bwanji munthu wina.”​—Kiana.