Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Ndingatani Ngati Anthu Ena Amandivutitsa pa Intaneti?

Ndingatani Ngati Anthu Ena Amandivutitsa pa Intaneti?

 Zimene muyenera kudziwa

 Intaneti imachititsa kuti anthu ena azivutitsa anzawo mosavuta. Buku lina linati: “Intaneti imachititsa ana omwe ndi akhalidwe labwino kukhala a mwano chifukwa chakuti palibe amene akuwaona.​—CyberSafe.

 Pali gulu lina la anthu limene limavutitsidwa kwambiri. Anthu oterewa angakhale amene amaoneka kuti ndi amanyazi, osamasuka kucheza ndi anthu kapenanso omwe amadzidelera.

 Kuvutitsidwa pa intaneti kumayambitsa mavuto aakulu. Kumachititsa anthu ena kuyamba kuvutika maganizo ndi kusowa ocheza nawo, ndipo nthawi zina anthu ena amafuna kudzipha.

 Zimene mungachite

 Dzifunseni kaye kuti, ‘Kodi ndikuvutitsidwadi?’ Nthawi zina anthu amanena zinthu zopsetsa mtima koma sikuti amafuna kupsetsadi mtima anzawo. Zimenezi zikachitika, tingachite bwino kutsatira malangizo a m’Baibulo awa:

 “Usamafulumire kukwiya mumtima mwako, pakuti anthu opusa ndi amene sachedwa kupsa mtima.”​—Mlaliki 7:9.

 Koma munthu wovutitsa ena ndi amene mwadala amachitira ena nkhanza, kuwachititsa manyazi kapenanso kuwaopseza kudzera pa intaneti.

 Ngati anthu amakuvutitsani pa intaneti muzikumbukira mfundo iyi: Zimene mumachita kapena kuyankha akakuvutitsani zingachititse kuti asiye kapena apitirize kukuvutitsani. Tayeserani kuchita chinthu chimodzi kapena zingapo zotsatirazi.

 Muzingonyalanyaza amene akukuvutitsaniyo. Baibulo limati: “Munthu wozindikira amakhala wofatsa.”​—Miyambo 17:27.

 Malangizowa ndi oona chifukwa wolemba mabuku wina dzina lake Nancy Willard analemba kuti: “Cholinga chachikulu cha anthu omwe amavutitsa anzawo pa intaneti ndi chofuna kuwakhumudwitsa. Ndipo kuti munthuyo akakhumudwadi, zimakhala ngati wawapatsa mphamvu zoti apitirize kumuvutitsa.”​—Cyberbullying and Cyberthreats.

 Mfundo yofunika kwambiri: Nthawi zina zimakhala bwino kungokhala chete.

 Muzipewa mtima wofuna kubwezera. Baibulo limanena kuti: “Osabwezera choipa pa choipa kapena chipongwe pa chipongwe.”—1 Petulo 3:9.

 Malangizowa ndi oona chifukwa buku lina linanena kuti: “Kukwiya kumasonyeza kuti munthuyo ndi wopanda mphamvu ndipo anthu okonda kuvutitsa anzawo amapezerera anthu oterewa. (Cyber-Safe Kids, Cyber-Savvy Teens) Komano kubwezera kulinso ndi mavuto ake chifukwa wovutitsidwawe umakhalanso ngati uli m’gulu la anthu omwe amakonda kuvutitsa anzawo.

 Mfundo yofunika kwambiri: Musamachite zinthu zomwe zingakulitse vutolo.

 Muyenera kuchitapo kanthu. Baibulo limati: “Musalole kuti choipa chikugonjetseni.” (Aroma 12:21) Mungathe kuchita zinazake kuti wokuvutitsaniyo asiye koma popanda kukulitsa vutolo.

 Mwachitsanzo:

  •    Pangani zoti musamathenso kulandira mameseji kuchokera kwa munthu amene amakuvutitsaniyo. Buku lina linati: “Sizingatheke kupsa mtima ndi zinthu zimene sunaziwerenge.”​—Mean Behind the Screen.

  •   Muzisunga zinthu zimene akutumizirani monga umboni ngakhale musaziwerenge. Zimenezi zingakhale mauthenga okulalatirani a pafoni, maimelo, mameseji a mawu kapena a mtundu wina uliwonse.

  •   Muziuza munthu amene amakuvutitsaniyo kuti asiye. Mungamutumizire meseji ngati yakuti:

    •  “Usanditumizirenso mameseji ena.”

    •  “Chotsa zimene wanditumizirazo.”

    •  “Ngati susiya zimenezi ndipeza njira zina zothetsera vutoli.”

  •   Musamadzidelere. M’malo momangoganizira zimene mukulephera, muziganizira kwambiri zomwe mumachita bwino. (2 Akorinto 11:6) Anthu okonda kuvutitsa ena pa intaneti nawonso amakonda anthu ooneka ngati amantha.

  •   Uzani munthu wina wamkulu. Mungayambe n’kuuza makolo anu. Mungachitenso bwino kufotokozera eniake a webusaiti yomwe munthu wokuvutitsaniyo akugwiritsa ntchito. Ngati zafika poipa kwambiri, inu ndi makolo anu muyenera kukanena zomwe zikuchitikazo ku sukulu, ku polisi kapenanso kupempha a zamalamulo kuti akuthandizeni.

 Mfundo yofunika kwambiri: Pali zinthu zimene mungachite kuti anthu asiye kukuvutitsani kapenanso kuti musamavutitsidwe kwambiri.