ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupewa Kunama ndiponso Kuba?
N’chifukwa chiyani anthu ena amanama komanso kuba?
Masiku ano anthu ambiri amaona kuti munthu sizingamuyendere ngati sachita chinyengo. Ena angamaganize kuti:
‘Ndikapanda kunamiza makolo anga, akhoza kundipatsa chilango.’
‘Ndikapanda kubera mayeso, ndilephera.’
‘Ndikapanda kuba chinthuchi, ndifunikira kusunga ndalama kuti ndidzachigule.’
Anthu ena angamadzifunse kuti, ‘N’zoona kuti n’kulakwadi kuchita zimenezi? Ndimakhulupirira kuti aliyense amachita zinthu zimenezi.’
Komabe izi si zoona. Anthu ambiri, ngakhalenso achinyamata, amakhulupirira kuti kupewa kunama ndiponso kuba n’kothandiza kwambiri. Baibulo limati: “Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.” (Agalatiya 6:7) Choncho zimene timachita zimakhala ndi zotsatirapo zabwino kapena zoipa.
Tiyeni tione mavuto amene anthu akumana nawo chifukwa chonena mabodza.
“Ndinanamiza mayi anga n’kuwauza kuti sindinalankhule ndi mnyamata winawake. Mayi angawa anali ndi umboni woti ndinkanama. Nditawanamiza kachitatu mayi anakhumudwa kwambiri. Anandiuza kuti ndisacheze ndi aliyense kwa milungu iwiri ndiponso kuti ndisagwiritse ntchito foni yanga kapena kuonera TV kwa mwezi umodzi. Kuyambira nthawiyo, sindinawanamizenso.”—Anita.
Zoti muganizire: N’chifukwa chiyani zingatenge nthawi kuti mayi a Anita ayambirenso kumukhulupirira?
Zimene Baibulo limanena: “Popeza tsopano mwataya chinyengo, aliyense wa inu alankhule zoona kwa mnzake.”—Aefeso 4:25.
“Ndinanamiza makolo anga ndipo ndinaganiza kuti ndawapusitsa. Koma kenako anandifunsanso zimene zinachitika. Ndinalephera kuwafotokozera zofanana ndi zimene ndinanena poyamba chifukwa zinali zabodza zokhazokha moti pa nthawiyo ndinali nditaziiwala. Sindikanavutika kukumbukira zikanakhala kuti zimene ndinawauzazo zinali zoona.—Anthony.
Zoti muganizire: Kodi Anthony akanapewa bwanji vutoli?
Zimene Baibulo Limanena: “Milomo yonama imam’nyansa Yehova, koma anthu ochita zinthu mokhulupirika amam’sangalatsa.”—Miyambo 12:22.
Mnzanga wina amakonda kwambiri kukokomeza nkhani. Amatha kusintha kapena kuwonjezera zinthu zina n’cholinga choti nkhani ikome. Ndimamukonda kwambiri ndipo sindimamutengera. Koma zimandivuta kuti ndizimukhulupirira kapena kumudalira.”—Yvonne.
Zoti muganizire: Kodi zimenezi zingawononge bwanji mbiri ya mnzake wa Yvonne?
Zimene Baibulo limanena: “Tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.”—Aheberi 13:18.
N’chifukwa chiyani kupewa kunama ndiponso kuba n’kothandiza?
Tiyeni tsopano tione zotsatirapo zabwino za kupewa kunama ndiponso kuba.
“Mayi wina amene ankayenda kutsogolo kwanga anagwetsa ndalama. Ndinamuimitsa n’kubweza ndalama zake. Iye anayamikira. Anati: ‘Wachita bwino kwambiri. Anthu ambiri akanangotola n’kuthyolera m’thumba.’ Ndinasangalala kuti anandiyamikira chifukwa chochita zabwino.—Vivian.
Zoti muganizire: N’chifukwa chiyani mayiyo anadabwa kwambiri kuti Vivian anabweza ndalama zake? N’chifukwa chiyani Vivian anasangalala ndi zimene anachitazo?
Zimene Baibulo Limanena: “Odala ndi anthu amene . . . [amachita ] zolungama nthawi zonse.”—Salimo 106:3.
“Tonse a m’banja lathu timagwira ntchito yokonza m’maofesi. Nthawi zina tikamakonza m’maofesi timapeza kandalama kenakake kamene kagwera pansi. Izi zikachitika timatola kandalamako n’kukaika padesiki yomwe ili pafupi. Munthu wina wogwira ntchito mu ofesi inayake ataona zimenezi anadabwa n’kunena kuti, ‘Bwanji mukuvutika kubweza kandalama kochepaka.’ Ngakhale kuti sanatimvetse, munthuyo amatikhulupirira kwambiri.”—Julia.
Zoti muganizire: Ngati Julia akufuna kukalowa ntchito kwina, kodi mabwana ake angamulembere zinthu zotani pa nkhani ya kukhala wokhulupirika?
Zimene Baibulo limanena: “Chita chilichonse chotheka kuti usonyeze kuti ndiwe wovomerezeka pamaso pa Mulungu, wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi.”—2 Timoteyo 2:15.
“Ndinalandira ndalama zokwana kugwira ntchito maola 80 koma ndinali nditangogwira ntchito maola 64 okha. Ndikanasangalala kulandira ndalama zonsezi koma ndinkadziwa kuti ndiyenera kuzibweza. Ndinauza munthu woyang’anira zandalama zimene zachitika ndipo anayamikira kwambiri. Ngakhale kuti kampaniyi ndi yochita bwino, sindikanatenga ndalama zimene si zanga chifukwa kuchita zimenezi ndi kuba.”—Bethany.
Zoti muganizire: Kodi kubera munthu n’kulakwa kuposa kubera kampani?
Zimene Baibulo limanena: “Munthu wochita zachiphamaso Yehova amanyansidwa naye, koma amakonda anthu owongoka mtima.”—Miyambo 3:32.