ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA
N’chifukwa Chiyani Ndimadzivulaza?
Kodi kudzivulaza kumene tikukambirana m’nkhaniyi n’kutani?
Kudzivulaza kumene tikukambirana m’nkhaniyi ndi khalidwe lokonda kudzicheka mwadala. Kuwonjezera pa kudzicheka, anthu ena amadziwotcha kapenanso kudzimenya. Ngakhale kuti nkhaniyi ikufotokoza kwambiri za kudzicheka, mfundo zake n’zothandizanso kwa anthu amene amakonda kudzivulaza mwadala m’njira zina.
Mukudziwa zotani pa nkhaniyi: Kodi mfundo zotsatirazi n’zoona kapena zonama?
Atsikana okha ndi amene amadzivulaza.
Khalidwe lodzicheka ndi lotsutsana ndi lamulo la m’Baibulo la pa Levitiko 19:28, limene limati: “Musamadzicheke.”
Mayankho olondola:
Zonama. Ngakhale kuti zikuoneka kuti anthu ambiri amene ali ndi vutoli ndi atsikana, anyamata ena nawonso amadzicheka kapena kudzivulaza m’njira zina.
Zonama. Lemba la Levitiko 19:28 likunena za zimene zinkachitika pa mwambo wakale wa anthu olambira milungu yonyenga, osati khalidwe lokonda kudzivulaza limene tikukambirana m’nkhaniyi. Komabe, n’zomveka kuganiza kuti Mlengi wathu safuna kuti tidzidzivulaza mwadala.—1 Akorinto 6:12; 2 Akorinto 7:1; 1 Yohane 4:8.
N’chifukwa chiyani anthu ena amachita zimenezi?
Mukudziwa zotani pa nkhaniyi: Kodi ndi mfundo iti imene mukuganiza kuti ndi yolondola kwambiri?
Anthu amadzicheka chifukwa . . .
chovutika maganizo.
amakhala akufuna kudzipha.
Yankho lolondola: A. Anthu ambiri amene amadzivulaza sikuti amafuna kudzipha. Iwo amangodzivulaza pofuna kuti amveko bwino chifukwa chovutika maganizo.
Taonani zimene achinyamata ena omwe ali ndi vuto lodzicheka ananena.
Celia: “Ndikadzicheka, ndimamvako bwino.”
Tamara: “Zimandithandiza ndithu. Ululu umene ndimamva ndikadzicheka ndi wabwino poyerekeza ndi umene ndimamva ndikamavutika maganizo.”
Carrie: “Nkhawa zimandisowetsa mtendere. Ululu umene ndimamva ndikadzicheka umandithandiza kuti ndiiwaleko mavuto.”
Jerrine: “Nthawi iliyonse ndikadzicheka, ndimamva bwino kwambiri chifukwa ndimaiwaliratu mavuto anga onse.”
Ngati muli ndi vutoli, kodi mungatani kuti musiye?
Kupemphera kwa Yehova Mulungu kungakuthandizeni kwambiri kuti muthane ndi vutoli. Baibulo limati: “[Mumutulire] nkhawa yanu yonse pakuti Iye asamalira inu.”—1 Petulo 5:7, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.
Yesani izi: Yambani ndi mapemphero afupiafupi. Mwina mungapemphere mwachidule kwa Yehova kuti, “Chonde, ndithandizeni.” M’kupita kwa nthawi, mudzayamba kulankhula zambiri m’pemphero lochokera pansi pa mtima lopita kwa “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse.”—2 Akorinto 1:3, 4.
Koma pemphero sikuti langokhala chinthu chimene chingakuthandizeni kuti mumveko bwino kwa nthawi yochepa. Pemphero ndi njira yodalirika imene mungalankhulire ndi Atate wanu wakumwamba, yemwe akukulonjezani kuti: “Ndithu ndikuthandiza. Ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lachilungamo.”—Yesaya 41:10.
Anthu ambiri amene anali ndi vuto lodzicheka anathandizidwanso atalankhula ndi makolo awo kapena munthu wamkulu amene iwowo amamukhulupirira. Taonani zimene atsikana atatu ananena atadziwitsa vuto lawoli makolo awo kapena anthu ena achikulire.
Mafunso ofunika kuwaganizira
Mukakhala wokonzeka kuuza ena za vuto lanu kuti akuthandizeni, kodi mungauze ndani?
Kodi mungamuuze zotani Yehova Mulungu pa vuto lanulo?
Kodi mungatchule zinthu ziwiri (kupatulapo kudzivulaza) zomwe mungachite kuti mumveko bwino mukakhala ndi nkhawa kapena mukamavutika maganizo kwambiri?