ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA
N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupepesa?
Kodi mungatani pazochitika zotsatirazi?
Aphunzitsi anu akukukalipirani chifukwa chochita zinthu zosokoneza m’kalasi.
Kodi muyenera kuwapepesa ngakhale mukuona kuti angokulitsa nkhaniyo?
Mnzanu wamva kuti mumamunena.
Kodi muyenera kumupepesa ngakhale mukudziwa kuti zomwe munanenazo ndi zoona?
Bambo anu akukhumudwitsani ndipo mukuwayankhula mopanda ulemu.
Kodi muyenera kuwapepesa ngakhale mukudziwa kuti iwowo ndi amene anakukhumudwitsani?
Yankho la mafunso onsewa ndi lakuti inde. Koma n’chifukwa chiyani muyenera kupepesa ngakhale mukudziwa kuti munali ndi zifukwa zomveka zochitira zomwe munachitazo?
N’chifukwa chiyani muyenera kupepesa?
Kupepesa kumasonyeza kuti mukukula. Mukapepesa chifukwa cha zimene munachita kapena kunena, mumasonyeza kuti muli ndi makhalidwe abwino amene angakuthandizeni mukadzakula.
“Kuti munthu apepese komanso kumvetsera zimene wina akunena, amafunika kukhala wodzichepetsa komanso woleza mtima.”—Rachel.
Kupepesa kumathandiza kuti muzikhala pamtendere ndi ena. Anthu amene amapepesa amasonyeza kuti nkhawa yawo yaikulu ndi kukhazikitsa mtendere osati kusonyeza kuti wolakwa ndi ndani.
“Ngakhale mukuona kuti simunalakwe, cholinga chanu chachikulu chizikhala kukhazikitsa mtendere. Sizifuna ndalama kuti munthu apepese koma zimathandiza kuti munthu ayambe kugwirizananso ndi anzake.”—Miriam.
Kupepesa kumathandiza kuti mukhale ndi mtendere wamumtima. Ukakhumudwitsa munthu wina chifukwa cha zomwe walankhula kapena kuchita sumamva bwino. Koma ukapepesa umakhala ngati watula chimtolo cholemetsa. a
“Ndimakumbukira kuti nthawi zina sindinkalankhula bwino ndi mayi kapena bambo anga. Zimenezi zinkandisowetsa mtendere koma ndinkavutika kuwapepesa. Koma ndikapepesa, ndinkamva bwino chifukwa zinkathandiza kuti m’banja mwathu mukhale mtendere.”—Nia.
Kodi zimachita kufunika khama kuti munthu upepese? Inde. Mtsikana wina wazaka 26 dzina lake Dena anafunika kupepesa mayi ake maulendo angapo chifukwa chochita zinthu mopanda ulemu. Iye ananena kuti: “Zimakhala zovuta kunena kuti ‘pepani.’ Ndimangoona ngati chinachake chandiima pakhosipa ndipo mawu sangatuluke.”
Kodi mungapepese bwanji?
Muzipepesa pamasom’pamaso ngati n’zotheka. Kuchita zimenezi kumathandiza kuti munthu winayo aone kuti mukumupepesadi kuchokera pansi pa mtima. Zingakhale zovuta kukukhulupirirani ngati mutapepesa polemba meseji. Ngakhale mutaika timaimoji tosonyeza nkhope yachisoni pameseji yomwe mwalembayo, sizingasonyeze kuti mukupepesa kuchokera pansi pa mtima.
Zimene zingakuthandizeni: Ngati simungakwanitse kupepesa pamasom’pamaso, mukhoza kuimba foni kapena kulemba kadi. Pa njira iliyonse yomwe mungagwiritse ntchito, muzisankha bwino mawu.
Mfundo ya m’Baibulo: “Mtima wa munthu wolungama umayamba waganiza usanayankhe.”—Miyambo 15:28.
Muzipepesa mofulumira. Mukachedwa kupepesa, vutolo limangokulirakulirabe ndipo zimakhala zovuta kuchita zinthu momasuka ndi munthu amene mwamulakwira.
Zimene zingakuthandizeni: Dziikireni cholinga. Mwachitsanzo, ‘Ndikufuna kupepesa lero.’ Ganizirani nthawi yomwe mukufuna kukapepesa ndipo musalephere kuchita zimenezi.
Mfundo ya m’Baibulo: “Thetsa nkhani mofulumira.”—Mateyu 5:25.
Muzipepesa kuchokera pansi pa mtima. Kunena kuti, “Pepa ngati ukuona kuti ndakukhumudwitsa,” si kupepesa mochokera pansi pa mtima. Mtsikana wina dzina lake Janelle anati: “Nthawi zambiri munthu amene munamulakwira angakulemekezeni akaona kuti mukuvomereza kuti munamulakwiradi.”
Zimene zingakuthandizeni: Musamayembekezere kuti mnzanuyo achite kaye mbali yake kuti mumupepese. Musamanene kuti, “Ndimupepesa pa zimene ndamulakwira iyenso akandipepesa pa zimene wandilakwira.”
Mfundo ya m’Baibulo: “Tiyeni titsatire zinthu zobweretsa mtendere.”—Aroma 14:19.
a Mukawononga kapena kutaya chinthu cha munthu wina, zingakhale bwino kulipira kapena kukonzetsa zomwe mwawonongazo kuwonjezera pa kupepesa.