Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Zimene Zingakuthandizeni Mukatha Msinkhu

Zimene Zingakuthandizeni Mukatha Msinkhu

 “Pamakhala mavuto ambiri mtsikana akangotha msinkhu. Zimapweteka, umadziona ngati wauve, komanso umabalalika. Tingati umaona kuti chilichonse n’choipa.”​—Oksana.

 “Ndinkati ndikasangalala, pasanapite nthawi ndinkapezeka kuti ndakhumudwa. Sindikudziwa ngati zimenezi zimachitikiranso anyamata ena koma ineyo zinkandichitikira.”​—Brian.

 Zimene zimachitika munthu akatha msinkhu tingaziyerekezere ndi zimene zimachitika ukamatsika malo otsetsereka kwambiri utakwera njinga. Zimakhala zosangalatsa koma zochititsa mantha. Ndiye kodi mungapirire bwanji mavuto amene amakhalapo munthu akatha msinkhu?

 Kodi kutha msinkhu n’kutani?

 Kunena mwachidule, kutha msinkhu ndi nthawi imene maganizo komanso thupi la munthu zimayamba kusintha kwambiri posonyeza kuti akukula. Pa nthawiyi, thupi lanu limayamba kukhwima kuti mudzathe kubereka.

 Komatu zimenezi sizikutanthauza kuti mumakhala mutafika msinkhu woti n’kukhala ndi mwana. Kutha msinkhu kumangokhala chizindikiro chakuti mwachoka ku umwana ndipo mukukula. Zinthu zina zimene zimasintha pa nthawiyi zingakhale zosangalatsa koma zina zingakukhumudwitseni.

 Kuyankha Mafunso: Tchulani zaka zimene munthu ayenera kutha msinkhu.

  • 8

  • 9

  • 10

  • 11

  • 12

  • 13

  • 14

  • 15

  • 16

 Yankho: Zaka zonsezi zikhoza kukhala zoyenera kuti munthu athe msinkhu.

 Choncho simuyenera kuda nkhawa ngati mwafika zaka 15 kapena 16 koma simunathe msinkhu. Komanso simuyenera kuda nkhawa ngati simunakwanitse zaka 10 koma mwatha kale msinkhu. Munthu aliyense amatha msinkhu pa zaka zosiyana ndi wina.

Mofanana ndi kukwera chinjinga pamtsetse, kutha msinkhu kukhoza kukhala kosangalatsa komanso kochititsa mantha. Komabe mukhoza kupirira mavuto amene amakhalapo pa nthawiyi

 Zimene zimasintha m’thupi

 Pa nthawiyi thupi limakula mofulumira. Koma vuto n’lakuti ziwalo zonse za thupi lanu sizikula pa nthawi yofanana. Izi zimachititsa kuti munthu azivutika kuchita zinthu zina bwinobwino. Koma musamadandaule, chifukwa nthawiyi ikadzadutsa vutoli lidzatha.

 Munthu akatha msinkhu, pamakhala zinthu zingapo zimene zimasintha.

 Zimene zimachitikira anyamata:

  •   Maliseche amakula

  •   Amamera ndevu ndiponso amamera tsitsi kukhwapa komanso malo ena

  •   Mawu amasintha

  •   Chilakolako chofuna kugonana chimakula ndipo nthawi zina amatha kutuluka umuna pogona

 Zimene zimachitikira atsikana:

  •   Amamera mabere

  •   Amamera tsitsi kukhwapa ndiponso malo ena

  •   Amayamba kusamba

 Zimene zimachitikira anyamata ndi atsikana omwe:

  •   Amayamba kutulutsa fungo chifukwa cha mabakiteriya amene amakhala m’thukuta.

     Zimene zingakuthandizeni: Mukhoza kuchepetsa fungolo mukamasamba kawirikawiri komanso kugwiritsa ntchito perefyumu kapena mankhwala oletsa thukuta.

  •   Amachita ziphuphu chifukwa choti mabakiteriya amatsekeredwa m’tiziwalo totulutsa mafuta pakhungu.

     Zimene zingakuthandizeni: Mukhoza kuchepetsa vutoli mukamasamba nkhope yanu pafupipafupi komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osalalitsa khungu.

 Kaganizidwe kamasintha

 Zinthu zimene zikusintha m’thupi lanu zingachititsenso kuti musinthe mmene mumachitira zinthu komanso kumvera. Nthawi zina kaganizidwe kanu kakhoza kumasinthasintha.

 “Umapezeka kuti tsiku lina ukungolira koma tsiku lotsatira uli bwinobwino. Nthawi ina umakwiya ndipo pena umangodzitsekera m’chipinda chifukwa cha nkhawa.”—Oksana.

 Pa nthawiyi, achinyamata ambiri amakhala ndi nkhawa chifukwa amaganiza kuti anthu onse akuyang’ana zimene akuchita ndipo akuwaganizira zoipa. Nkhawayi imakulanso chifukwa choti akusintha kwambiri mmene akuonekera.

 “Thupi langa litayamba kusintha, ndinkachita manyazi moti sindinkakonda kuima mowongoka ndipo ndinkavala zovala zazikulu. Ndinkadziwa chifukwa chake thupi langa likusintha komabe sizinkandisangalatsa ndipo ndinkangoona ngati si thupi langa.”—Janice.

 Chinanso chimene chimasintha kwambiri ndi mmene amaonera anthu amene si anyamata kapena atsikana anzawo.

 “Ndinasiya kuganiza kuti anyamata onse ndi ovuta. Ndinayamba kukopeka ndi anyamata ena moti ndinkaona kuti akhoza kukhala zibwenzi zanga. Ndikamacheza ndi anzanga, nkhani inkangokhala yofunsana kuti, ‘Kodi iwe amakusangalatsa ndi uti?’”​—Alexis.

 Pa nthawi imeneyi, achinyamata ena amatha kukopeka ndi munthu amene ndi mnyamata kapena mtsikana mnzawo. Izi zikakuchitikirani, musamaganize kuti ndi mmene zidzakhalire nthawi zonse. Tikutero chifukwa nthawi zambiri munthu akakula amasiya kukopeka ndi anyamata kapena atsikana anzake.

 “Nthawi zonse ndinkadziyerekezera ndi anyamata anzanga ndipo izi zinachititsa kuti ndiyambe kukopeka nawo. Koma patapita nthawi ndinayamba kukopeka ndi atsikana. Panopa sindikopekanso ndi anyamata anzanga.”​—Alan.

 Zoyenera kuchita

  •    Yesetsani kuona zinthu moyenera. Kusintha kumene kumachitika munthu akatha msinkhu n’koyenera pa moyo wa munthu aliyense. Mukhoza kulimbikitsidwa mukaganizira mawu amene Davide anauza Mulungu. Anati: “Munandipanga modabwitsa ndipo zimenezi zimandichititsa mantha.”—Salimo 139:14.

  •   Musamadziyerekezere ndi anthu ena ndipo musamaganizire kwambiri za kaonekedwe kanu. Paja Baibulo limati: “Munthu amaona zooneka ndi maso, koma Yehova amaona mmene mtima ulili.”—1 Samueli 16:7.

  •   Yesetsani kuchita masewera olimbitsa thupi ndiponso kupuma mokwanira. Kugona mokwanira kungakuthandizeni kuchepetsa vuto lopsa mtima, kukhala wokhumudwa kapena kuda nkhawa.

  •   Musamadzikayikire. Si zoona kuti anthu onse akuyang’ana zimene mukuchita. Musamadandaule anthu akanena zinthu zokhudza mmene mwasinthira. Baibulo limati: “Usamaganizire kwambiri mawu onse amene anthu amalankhula.”—Mlaliki 7:21.

  •   Yesetsani kukhala wodziletsa kuti chilakolako chofuna kugonana chisamakulamulireni. Baibulo limati: “Thawani dama. . . . Amene amachita dama amachimwira thupi lake.”—1 Akorinto 6:18.

  •   Kambiranani ndi makolo anu kapena munthu wina wachikulire yemwe mumamudalira. N’zoona kuti poyamba mungachite manyazi. Koma malangizo amene angakupatseni angakuthandizeni kwambiri.—Miyambo 17:17.

 Mfundo yofunika kwambiri: Munthu akatha msinkhu amakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Komabe pa nthawiyi munthu amakula m’njira zosiyanasiyana. Thupi lake limakula ndipo amayamba kuganiza ngati munthu wamkulu. Pa nthawiyi akhozanso kulimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova.—1 Samueli 2:26.