MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA
Kodi Mungasonyeze Bwanji Kuti Mumakonda Mwamuna Kapena Mkazi Wanu?
Zaka zikamadutsa, mabanja ena amayamba kuchepetsa chikondi chomwe ankasonyezana. Ngati zimenezi n’zomwe zikuchitika m’banja lanu, kodi muyenera kuda nkhawa?
Zimene muyenera kudziwa
Kusonyezana chikondi kumathandiza kuti mukhale ndi banja losangalala komanso lolimba. Kuti tikhale amphamvu komanso athanzi, timafunika kudya chakudya komanso kumwa madzi nthawi zonse. Zimenezi n’zofanananso ndi zimene zimafunika m’banja. Kuti mukhale ndi banja lolimba, muyeneranso kumasonyezana chikondi nthawi zonse. Ngakhale mwamuna ndi mkazi atakhala limodzi m’banja kwa zaka zambiri, aliyense amafuna kumva kuti mnzakeyo amamukonda kwambiri.
Chikondi chenicheni sichidzikonda. Zimenezi zikusonyeza kuti chikondi chimaganiziranso zofuna za ena. Choncho m’malo moti mwamuna kapena mkazi azisonyeza chikondi kwa mnzake chifukwa cha mmene waonera pa nthawiyo, amafunika kudziwa kuti mnzakeyo amafunika kusonyezedwa chikondi nthawi zonse.
Mwachibadwa, akazi amafuna kusonyezedwa chikondi kwambiri kuposa mmene zimakhalira ndi amuna. Mwamuna akhoza kumakonda kwambiri mkazi wake. Koma ngati amangomusonyeza chikondicho tsiku likamayamba kapena likamatha komanso pokhapokha ngati akufuna kugona naye, mkaziyo akhoza kumakayikira ngati mwamuna wakeyo amamukondadi. Choncho ndi bwino kuti nthawi zonse muzisonyeza kuti mumakonda mkazi wanu.
Zimene mungachite
Muzimulankhula mawu achikondi. Mwamuna kapena mkazi wanu amasangalala kwambiri mukamamuuza mawu ngati akuti “ndimakukonda” kapena akuti “ndiwe wofunika kwambiri kwa ine.”
Lemba lothandiza: “Pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima.”—Mateyu 12:34.
Zimene zingakuthandizeni: Musamamulankhule mawu a chikondi ndi pakamwa pokha. Nthawi zina mungamulembere mawuwo papepala kapena kumutumizira meseji.
Muzichita zinthu zosonyeza kuti mumamukonda. Kungouza mwamuna kapena mkazi wanu kuti mumamukonda, pakokha sikungakhale kokwanira. Ndibwinonso kuti nthawi zina muzimuhaga, kumukisa komanso kumugwira dzanja poyenda. Mungasonyezenso kuti mumakonda mnzanuyo, mukamamusisita, kumuyang’ana mwachikondi komanso kumugulirako kamphatso. Kodi mumapeza nthawi yothandiza mkazi wanu pa zinthu monga kumunyamulira chikwama, kumutsegulira chitseko, kutsuka mbale, kuchapa zovala kapenanso kumuthandiza kuphika? Ambiri amaona kuti kuchita zimenezi ndi njira ina yosonyezera kuti mumakonda kwambiri mkazi wanu.
Lemba lothandiza: “Tisamakondane ndi mawu okha kapena ndi pakamwa pokha, koma tizisonyezana chikondi chenicheni m’zochita zathu.”—1 Yohane 3:18.
Zimene zingakuthandizeni: Muzisonyeza kuti mumaganizira kwambiri mwamuna kapena mkazi wanu ngati mmene munkachitira muli pa chibwenzi.
Muzipeza nthawi yochitira zinthu limodzi. Kukhala awiriwiri n’kothandiza kwambiri m’banja. Kumathandizanso mnzanuyo kuona kuti mumasangalala kuchitira naye zinthu limodzi. N’zoona kuti ngati muli ndi ana komanso ngati tsiku lililonse mumatanganidwa ndi zochita zambiri, zingakhale zovuta kupeza nthawi yochita zinthu muli awiriwiri ndi mwamuna kapena mkazi wanuyo. Ngati ndi choncho, mwina mukhoza kungochita zinthu zina ngati kukawongola miyendo muli awiri basi.
Lemba lothandiza: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”—Afilipi 1:10.
Zimene zingakuthandizeni: Mabanja ena omwe mwamuna ndi mkazi wake amakhala otanganidwa kwambiri, amakonza nthawi yokadyera limodzi chakudya chamadzulo pamalo enaake. Amachita zimenezi kumapeto kwa wiki kapena tsiku lina lomwe akonza.
Muyenera kumudziwa bwino mnzanuyo. Aliyense amakhala ndi zomwe amakonda. Choncho muyenera kukambirana kuti aliyense afotokoze zomwe amafuna kuti mnzake azimuchitira pomusonyeza chikondi kapenanso ngati pangafunike zina zomwe mungamachite. Kenako yesetsani kuchita zomwe mnzanuyo amafuna. Musaiwale kuti kusonyezana chikondi kumathandiza kuti mukhale ndi banja losangalala komanso lolimba.
Lemba lothandiza: “Chikondi . . . sichisamala zofuna zake zokha.”—1 Akorinto 13:4, 5.
Zimene zingakuthandizeni: M’malo mokakamiza mwamuna kapena mkazi wanu kuti azikukondani, muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndichite chiyani kuti mwamuna kapena mkazi wangayu azindikonda?’