MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | BANJA
Kodi Mungatani Kuti Zipangizo Zamakono Zisamakusokonezeni?
Zipangizo zamakono zikhoza kulimbitsa kapena kusokoneza banja lanu. Kodi zimenezi zingachitike bwanji?
Zimene muyenera kudziwa
Kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono mwanzeru kukhoza kulimbitsa banja lanu. Mwachitsanzo, amuna ena ndi akazi awo, amagwiritsira ntchito zipangizozi polumikizana pa nthawi imene sali limodzi.
“Meseji yachidule yongonena kuti ‘ndimakukonda’ kapena ‘ndakusowa’ ingatanthauze zambiri ndipo imakupangitsa kumva bwino.”—Jonathan.
Kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono mopanda nzeru kukhoza kusokoneza banja lanu. Mwachitsanzo, anthu ena amangokhalira kucheza pa foni ndipo zimenezi zimachititsa kuti asamakhale ndi nthawi yokwanira yocheza ndi mwamuna kapena mkazi wawo.
“Sindikukayikira kuti pali nthawi zina pamene mwamuna wanga ankafuna atacheza nane, koma ankalephera chifukwa choti ndinkatanganidwa ndi foni.”—Julissa.
Anthu ena amaona kuti akhoza kumakambirana zinthu zofunika ndi mwamuna kapena mkazi wawo kwinakunso akugwiritsa ntchito chipangizo chawo chamakono. Koma Sherry Turkle, yemwe ndi katswiri wa zachikhalidwe anatsutsa mfundo imeneyi. Iye ananena kuti “n’zosatheka kumachita zinthu ziwiri pa nthawi imodzi, ndipo tikamachita zinthu zingapo pa nthawi imodzi m’pamene zambiri zimawonongeka.” a
“Ndimasangalala kwambiri kucheza ndi mwamuna wanga akakhala kuti sakuchita zinthu zina. Koma ndikamacheza naye, iyeyo n’kumatanganidwa ndi foni, zimakhala ngati foniyo ndi yofunika kwambiri kuposa ineyo.”—Sarah.
Mfundo yofunika kwambiri: Mmene mumagwiritsira ntchito zipangizo zamakono zingachititse kuti banja lanu likhale lolimba kapena lisokonezeke.
Zimene mungachite
Muzidziwa zinthu zofunika kwambiri. Baibulo limanena kuti: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.” (Afilipi 1:10) Dzifunseni kuti, ‘Kodi timatanganidwa kwambiri ndi zipangizo zamakono moti timasowa nthawi yocheza kapena yochitira zinthu limodzi?’
“Zimamvetsa chisoni ukaona mwamuna ndi mkazi wake aliyense ali pa foni pa nthawi yomwe akudya pa lesitanti. Sitikuyenera kukhala akapolo a mafoni mpaka kufika poiwala kuti mwamuna kapena mkazi wathu ndi amene ali wofunika kwambiri.”—Matthew.
Muzidziikira malire. Baibulo limanena kuti: “Samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera si monga anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru. Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.” (Aefeso 5:15, 16) Dzifunseni kuti, ‘Kodi sizingatheke kuti ndizikhala ndi nthawi yoti ndiziyankha mameseji osafunika kwenikweni m’malo moti ndizingoyankha meseji iliyonse ikafika?’
“Ndimaona kuti ndibwino kutchera foni yanga kuti isamamveke mawu ikamaitana, ndipo ndimayankha mameseji onse omwe ndalandira pa nthawi yomwe ndili ndi mpata. Si nthawi zambiri pamene pamabwera uthenga wadzidzidzi womwe umafunika kuyankha pompopompo.”—Jonathan.
Ngati zingatheke, musamachite zinthu za kuntchito muli kunyumba. Baibulo limanena kuti: “Chilichonse chili ndi nthawi yake.” (Mlaliki 3:1) Dzifunseni mafunso awa: ‘Kodi ndimalephera kucheza ndi banja langa ndikakhala kunyumba chifukwa choti ndimagwirabe ntchito pachipangizo chamakono? Ngati ndi choncho, kodi zimakhudza bwanji banja langa? Kodi mwamuna kapena mkazi wanga amati chani?’
“Zipangizo zamakono zimatithandiza kuti tizigwira ntchito nthawi ina iliyonse. Koma ndikakhala ndi mkazi wanga ndimayesetsa kuti ndisamangokhalira kuona pafoni n’kumatanganidwa ndi zinthu za kuntchito.”—Matthew.
Muzikambirana za mmene mumagwiritsira ntchito zipangizo zamakono. Baibulo limanena kuti: “Aliyense asamangodzifunira zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina.” (1 Akorinto 10:24) Muzikambirana ndi mwamuna kapena mkazi wanu za mmene mumagwiritsira ntchito zipangizo zamakono ndiponso ngati mungafunikire kusintha. Mungagwiritse ntchito gawo lakuti, mafunso oti mukambirane lomwe lili m’munsimu.
“Ine ndi mwamuna wanga timachenjezana tikaona kuti wina akugwiritsa ntchito kwambiri foni kapena tabuleti yake. Timadziwa kuti zimenezi zikhoza kuyambitsa mavuto, choncho timayesetsa kutsatira mosamala malangizo omwe winayo watipatsa.”—Danielle.
Mfundo yofunika kwambiri: Musamalole kuti zipangizo zamakono zizikulamulirani.
a Kuchokera m’buku lakuti, Reclaiming Conversation—The Power of Talk in a Digital Age.