Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi Baibulo N’chiyani?

Kodi Baibulo N’chiyani?

Yankho la M’Baibulo

 Baibulo ndi buku limene linapangidwa ndi mabuku ang’onoang’ono 66. Linalembedwa pa nthawi ya zaka pafupifupi 1,600. Baibulo lili ndi uthenga wochokera kwa Mulungu ndipo limadziwika kuti “mawu a Mulungu.”​—1 Atesalonika 2:13.

Zimene zili munkhaniyi

 Zoona zake zokhudza Baibulo

  •   Kodi analemba Baibulo ndi ndani? Mulungu ndi amene analemba Baibulo koma anagwiritsa ntchito amuna pafupifupi 40 kuti alilembe. Ena mwa anthuwa ndi Mose, Mfumu Davide, Mateyu, Maliko, Luka ndi Yohane. a Mulungu ndi amene anathandiza amunawa kulemba maganizo ake, choncho zonse zimene analemba ndi uthenga wochokera kwa Mulungu.​—2 Timoteyo 3:16.

     Mwachitsanzo: Ngati bwana akufuna kutumiza uthenga kwinakwake, amauza sekilitale wake kuti alembe kalata kapena imelo. Ngakhale kuti sekilitale ndi amene walemba koma uthengawo umakhala wa bwanayo. N’chimodzimodzinso ndi Baibulo. Ngakhale kuti anthu ndi amene analemba Baibulo koma uthenga wake ndi wochokera kwa Mulungu. Choncho, Mlembi Wamkulu wa Baibulo ndi Mulungu.

  •   Kodi mawu akuti “Baibulo” amatanthauza chiyani? Mawu akuti “Baibulo” amachokera ku mawu a Chigiriki akuti biblia, omwe amatanthauza “mabuku ang’onoang’ono.” Patapita nthawi, mawu akuti biblia anayamba kuimira Baibulo lomwe linali litapangidwa ndi mabuku ang’onoang’ono onse.

  •   Kodi Baibulo linalembedwa liti? Baibulo linayamba kulembedwa mu 1513 B.C.E., ndipo linamalizidwa cha m’ma 98 C.E., pambuyo pa zaka zoposa 1,600.

  •   Kodi Baibulo loyambirira lili kuti? Mabuku a Baibulo amene anayambirira kulembedwa sakupezeka masiku ano. Izi zili choncho chifukwa chakuti olemba Baibulo kalelo ankalilemba pa zinthu zosachedwa kuwonongeka monga gumbwa komanso zikopa. Komabe, akatswiri olemba mabuku ankakopera mawu a m’Baibulo mobwerezabwereza n’cholinga choti anthu ena m’tsogolo adzathe kuwerenga mawu a m’Baibulo.

  •   Kodi mawu akuti “Chipangano Chakale” ndi “Chipangano Chatsopano” amatanthauza Chiyani? Mbali ya Baibulo imene imadziwika kuti Chipangano Chakale, ndi chigawo cha Baibulo chimene chinalembedwa mu Chiheberi, b ndipo chimadziwikanso kuti Malemba Achiheberi. Pamene Chipangano Chatsopano, ndi chigawo cha Baibulo chomwe chinalembedwa mu Chigiriki, ndipo chimadziwikanso kuti Malemba Achigiriki. Zigawo ziwirizi ndi zimene zimapanga Baibulo lathunthu lomwe limadziwikanso kuti Malemba Opatulika. c

  •  Kodi m’Baibulo muli zotani? Mbali zosiyanasiyana za Baibulo zili ndi mbiri yakale, malamulo, maulosi, ndakatulo, miyambi, nyimbo komanso makalata.​—Onani “ Mndandanda wa Mabuku a m’Baibulo.”

 Kodi Baibulo limanena zotani?

 Baibulo limayamba ndi kufotokoza mfundo zachidule zokhudza mmene Mulungu Wamphamvuyonse analengera kumwamba ndi dziko lapansi. Mulungu amatiuza dzina lake lakuti Yehova kudzera m’Baibulo ndipo amafuna kuti anthu onse amudziwe.​—Salimo 83:18.

 Baibulo limafotokoza kuti dzina la Mulungu linadetsedwa ndipo limafotokozanso zimene adzachite kuti aliyeretse.

 Baibulo limatiuza cholinga chimene Mulungu analengera anthu komanso dzikoli. Limanena mmene Mulungu adzathetsere mavuto onse amene anthu akukumana nawo.

 Baibulo lili ndi malangizo othandiza kuti tizikhala moyo wabwino. Mwachitsanzo, limatithandiza pa nkhani monga:

  •   Kukhala bwino ndi anzathu. “Choncho zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo. Zimenezi ndi zomwe Chilamulo chimafuna komanso zimene aneneri analemba.”​—Mateyu 7:12.

     Tanthauzo lake: Zimene timafuna kuti ena atichitire, ifenso tiziwachitira zomwezo.

  •   Kuthana ndi nkhawa. “Musamadere nkhawa za mawa, chifukwa mawalo lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso.”​—Mateyu 6:34.

     Tanthauzo lake: Tisamadandaule zokhudza mavuto omwe angadzachitike m’tsogolo, koma tizingothana ndi mavuto amene tikukumana nawo panopa basi.

  •   Kukhala ndi banja losangalala. “Aliyense wa inu azikonda mkazi wake ngati mmene amadzikondera yekha komanso mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.”​—Aefeso 5:33.

     Tanthauzo lake: Chikondi komanso ulemu ndi makhalidwe ofunika kwambiri kuti anthu okwatirana azikhala mosangalala.

 Kodi Baibulo linasinthidwa?

 Ayi. Akatswiri a Baibulo akhala akuyerekezera mipukutu yakale ya Baibulo ndi Baibulo lomwe lilipo masiku ano ndipo apeza kuti uthenga wake woyambirira sunasinthidwe. Ndipotu zimenezi ndi zomveka, chifukwa Mulungu amafuna kuti anthu aziwerenga ndi kumvetsa uthenga wake. Choncho iye anaonetsetsa kuti uthenga wakewu usasinthidwe ngakhale pang’ono. d​—Yesaya 40:8.

 N’chifukwa chiyani pali Mabaibulo osiyanasiyana omwe anamasuliridwa?

 Baibulo lili ndi “uthenga wabwino” wa anthu “kudziko lililonse, fuko lililonse, chilankhulo chilichonse ndi mtundu uliwonse.” (Chivumbulutso 14:6) Komabe, masiku ano anthu ambiri sangamve zinenero zimene Baibulo linalembedwamo poyambirira. Pa chifukwa chimenechi, anthu amafunikira Baibulo lomasuliridwa m’chinenero chimene angamvetse bwino kuti azitha kuwerenga mawu a Mulungu ndi kuwamvetsa bwino.

 Omasulira Baibulo amatsatira njira zitatu izi:

  •   Kumasulira liwu ndi liwu potengera ndendende mmene chinenero chomwe akumasuliracho chalembedwera ngati n’zotheka kutero.

  •   Kumasulira mfundo pogwiritsa ntchito mawu omwe akumveketsa bwino mfundo ya chinenero choyambirira.

  •   Kumasulira mochita kufotokozera ndi cholinga chofuna kumveketsa bwino mfundo yake kuti owerenga azisangalala powerenga. Komabe, nthawi zina njira imeneyi imachititsa kuti tanthauzo la nkhani lisinthe chifukwa omasulira amakhala ndi ufulu wokometsera nkhaniyo.

 Kuti Baibulo likhale lomveka bwino, omasulira samafunika kungolimasulira liwu ndi liwu koma amafunikiranso kugwiritsa ntchito mawu omveka bwino mogwirizana ndi mmene anthu a munthawi yawo akulankhulira, n’cholinga choti azimva uthenga wa Mulungu molondola. e

 Ndi ndani amene anasankha zinthu zoti zilembedwe m’Baibulo?

 Monga Mlembi Wamkulu, Mulungu ndi amene anasankha zinthu zoti anthu alembe m’Baibulo. Poyamba “mawu opatulika a Mulungu anaikidwa mʼmanja mwa” mtundu wakale wa Aisiraeli chifukwa ndi amene Mulungu anawasankha kuti agwire ntchito yolemba Malemba Achiheberi.​—Aroma 3:2.

 Kodi pali mabuku ena amene akusoweka m’Baibulo?

 Ayi. Baibulo ndi lokwanira ndithu; palibe buku ngakhale limodzi limene “likusowekamo.” Anthu ena anganene kuti mabuku ena akale amene apezeka chaposachedwapa anali a m’Baibulo. f Komabe, zimene Baibulo limanena zili ngati muyezo wotithandiza kudziwa kuti ndi lokwanira bwino komanso ndi lolondola. (2 Timoteyo 1:13) Tikagwiritsa ntchito muyezo umenewu timapeza kuti mabuku onse a m’Baibulo ndi ouziridwa ndi Mulungu ndipo ndi ogwirizana. Zimenezi n’zosiyana ndi mabuku ena akale amene anthu ena amanena kuti nawonso ndi a m’Baibulo. g

 Mmene mungapezere mavesi m’Baibulo

  Mndandanda wa mabuku a m’Baibulo

a Kuti mudziwe zokhudza mndandanda wa mabuku onse a m’Baibulo, amene analemba komanso nthawi imene anamaliza kuwalemba, onani “Mabuku a M’Baibulo ndi Tsatanetsatane Wake.”

b Tizigawo ta Baibulo tolembedwa mu Chiaramu, chomwe ndi chofananako ndi Chiheberi.

c Anthu ambiri amakonda kutchula zigawo ziwiri za Baibulo ndi mawu akuti “Malemba Achiheberi” komanso “Malemba Achigiriki.” Zili choncho chifukwa chakuti mawuwa sachititsa munthu kuganiza kuti “Chipangano Chakale” chinatha ntchito ndipo chinalowedwa m’malo ndi “Chipangano Chatsopano.”

e Anthu ambiri amakonda kuwerenga Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika chifukwa linamasuliridwa molondola ndiponso ndi losavuta kuwerenga. Onani nkhani yakuti “Kodi Baibulo la Dziko Latsopano Linamasuliridwa Molondola?

f Mabuku amenewa onse pamodzi amatchedwa mabuku owonjezera a m’Baibulo (Apocrypha.) Malinga ndi zimene Encyclopædia Britannica imanena, “m’mabuku ofotokoza Baibulo, [mawu amenewa akutanthauza] mabuku osagwirizana ndi mndandanda wa mabuku ovomerezeka a Baibulo.” Zimenezi zikusonyeza kuti ndi osemphana ndi mabuku ovomerezeka a m’Baibulo.