Kodi Kukhululuka Kumatanthauza Chiyani?
Yankho la m’Baibulo
M’Baibulo mawu achigiriki amene anamasuliridwa kuti “kukhululuka” amatanthauza “kuiwala.” Zili ngati mmene munthu amachitira akakongoza munthu ndalama n’kungomusiya kuti asabwezenso ndalamazo. Yesu anauza ophunzira ake kuti azipemphera kuti: “Mutikhululukire machimo athu, pakuti nafenso timakhululukira aliyense amene amatilakwira.” (Luka 11:4) Ndiyeno mu fanizo lake lokhudza kapolo wopanda chifundo, Yesu anasonyeza kuti kukhululukira munthu wina kuli ngati kumukhululukira ngongole.—Mateyu 18:23-35.
Tikakhululukira munthu sitiyenera kusunga chakukhosi kapena kumayembekezera kuti achite zinazake zosonyeza kuti akupepesa. Baibulo limasonyeza kuti chikondi n’chimene chimathandiza munthu kukhululukira wina chifukwa limati chikondi “sichisunga zifukwa.”—1 Akorinto 13:4, 5.
Kukhululuka sikutanthauza zinthu izi:
Kulekerera zinthu zoipa. Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amadana ndi anthu amene amanena kuti zinthu zoipa n’zabwino ndipo zinthu zabwino n’zoipa.—Yesaya 5:20.
Kunyalanyaza zinthu zoipa. Mulungu anakhululukira Mfumu Davide atachita machimo aakulu koma sanamuteteze kuti asakumane ndi zotsatirapo za machimowo. Mulungu anachititsanso kuti machimowo alembedwe m’Baibulo, n’cholinga choti tiziphunzirapo.—2 Samueli 12:9-13.
Kulola kuti ena akuzolowereni. Tiyerekeze kuti mwakongoza munthu wina ndalama, ndiye munthuyo wawononga ndalamazo n’kumalephera kukubwezerani monga mmene analonjezera. Munthuyo akumva chisoni ndi zimene wachitazo ndipo akukupepesani. Mwina mungasankhe kusiya kuganizira nkhaniyo kapena kumukumbutsa ngongoleyo. Apo ayi mungasankhe kungomukhululukira basi. Komabe mukhozanso kusankha kuti musadzamubwerekenso ndalama.—Salimo 37:21; Miyambo 14:15; 22:3; Agalatiya 6:7.
Kukhululuka popanda chifukwa chomveka. Mulungu sakhululukira anthu amene amachimwa mwadala ndiponso amene safuna kusintha, kupepesa kapena kuvomereza kuti alakwa. (Miyambo 28:13; Machitidwe 26:20; Aheberi 10:26) Mulungu amadana ndi anthu osalapa amenewa ndipo sayembekezera kuti ifeyo tiwakhululukire.—Salimo 139:21, 22.
Koma bwanji ngati munthu wina wakulakwirani kwambiri koma akukana kupepesa kapena kuvomereza kuti walakwa? Baibulo limatipatsa malangizo pa nkhaniyi. Limati: “Usapse mtima ndipo pewa kukwiya.” (Salimo 37:8) Kuchita zimenezi sikutanthauza kunyalanyaza zolakwazo koma kungosiya kuganizira nkhaniyo. Muzikumbukira kuti munthuyo adzayankha mlandu kwa Mulungu. (Aheberi 10:30, 31) Muzikumbukiranso kuti posachedwapa Mulungu adzathetsa mavuto ndipo adzatithandiza kuti tisamadzavutikenso maganizo ndi zinthu zopweteka zimene zatichitikira.—Yesaya 65:17; Chivumbulutso 21:4.
Kukhululukira anthu amene sanatilakwire. Nthawi zina timafulumira kuganiza kuti munthu wina watilakwira pamene sanatilakwire n’komwe. Kuzindikira zimenezi kungakuthandizeni kuona kuti palibe chifukwa choti timukhululukire. Baibulo limanena kuti: “Usamafulumire kukwiya mumtima mwako, pakuti anthu opusa ndi amene sachedwa kupsa mtima.”—Mlaliki 7:9.
Kodi tingatani kuti tizikhululukira ena?
Tizikumbukira tanthauzo la kukhululuka. Kukhululuka sikutanthauza kulekerera kapena kunyalanyaza zolakwa koma kusiya kuganizira nkhaniyo.
Tiziganizira ubwino wa kukhululuka. Munthu amene saganizira zimene ena amulakwira, akhoza kukhala wathanzi, wachimwemwe ndiponso amakhala ndi mtendere wa mumtima. (Miyambo 14:30; Mateyu 5:9) Koma chofunika n’chakuti, tikamakhululukira ena, Mulungu amatikhululukiranso machimo athu.—Mateyu 6:14, 15.
Tizimvetsa ena akatilakwira. Tonse timalakwitsa zinthu. (Yakobo 3:2) Ndiye popeza timafuna kuti ena atikhululukire tikalakwitsa, nafenso tiyenera kuwakhululukira akatilakwira.—Mateyu 7:12.
Tizikhala ololera. Anthu akatilakwira zinthu zing’onozing’ono, tiyenera kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Pitirizani kulolerana.”—Akolose 3:13.
Tisachedwe kukhululuka. Yesetsani kukhululuka mwamsanga m’malo momangoganizira vutolo.—Aefeso 4:26, 27.