Kodi Mulungu Angayankhe Mapemphero Anga?
Yankho la m’Baibulo
Inde angayankhe. Baibulo limasonyeza zimenezi komanso anthu ena aona okha kuti Mulungu amayankha mapemphero. Baibulo limati: “Anthu amene amamuopa [Mulungu] adzawachitira zokhumba zawo, adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo ndipo adzawapulumutsa.” (Salimo 145:19) Kuti Mulungu ayankhe mapemphero anu zimadalira kwambiri pa zimene inuyo mumachita.
Zimene Mulungu amafuna
Muzipemphera kwa Mulungu osati kwa Yesu, Mariya, anthu oyera mtima, angelo kapena mafano. Yehova Mulungu yekha ndi amene ‘amamva pemphero.’—Salimo 65:2.
Muzipemphera mogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna zomwe zalembedwa m’Baibulo.—1 Yohane 5:14.
Muzipemphera m’dzina la Yesu chifukwa zimenezi zimasonyeza kuti mukuzindikira udindo wa Yesu. Paja iye anati: “Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.”—Yohane 14:6.
Musamakayikire zimene mukupempha ndipo nthawi zina mungapemphenso kuti akuwonjezereni chikhulupiriro.—Mateyu 21:22; Luka 17:5.
Muzipemphera kuchokera pansi pa mtima ndiponso modzichepetsa. Baibulo limati: “Ngakhale kuti Yehova ali pamwamba, amaona wodzichepetsa.”—Salimo 138:6.
Muzipemphera mwakhama. Paja Yesu anati: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani.”—Luka 11:9.
Zimene Mulungu saganizira poyankha
Mtundu kapena dziko lanu. “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”—Machitidwe 10:34, 35.
Mmene mwakhalira. Zilibe kanthu kuti mwakhala, mwagwada, mwawerama kapena mwaima.—1 Mbiri 17:16; Nehemiya 8:6; Danieli 6:10; Maliko 11:25.
Ngati mukupemphera motulutsa mawu kapena chamumtima. Mulungu amayankha mapemphero ngakhale amumtima.—Nehemiya 2:1-6.
Ngati nkhaniyo ndi yaing’ono kapena yaikulu. Mulungu akukulimbikitsani ‘kumutulira nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’—1 Petulo 5:7.