Kodi Baibulo Lingandithandize Kuti Ndisiye Kudziimba Mlandu?
Yankho la m’Baibulo
Inde. Baibulo lingatithandize kudziwa zoyenera kuchita kuti tisiye kudziimba mlandu. (Salimo 32:1-5) Tikalakwitsa zinazake n’kulapa mochokera pansi pamtima, Mulungu angatikhululukire n’kutithandiza kuti tisamadziimbe mlandu. (Salimo 86:5) Baibulo limasonyeza kuti nthawi zina kudziimba mlandu kungatithandize kuti tisiye kuchita zoipa komanso kuti tiyesetse kupewa kudzazichita m’tsogolo. (Salimo 51:17; Miyambo 14:9) Komabe, Baibulo limatichenjeza kuti tisamadziimbe mlandu mopitirira malire mwinanso n’kuyamba kudziweruza kuti ndife osafunika pamaso pa Mulungu. Kuchita zimenezi kungachititse kuti ‘timezedwe ndi chisoni.’—2 Akorinto 2:7.
N’chiyani chingachititse kuti ndizidziimba mlandu?
Pali zifukwa zosiyanasiyana zomwe zingatichititse kuti tiyambe kudziimba mlandu. Tikhoza kudziimba mlandu tikakhumudwitsa munthu amene timamukonda kapenanso tikalephera kutsatira mfundo zomwe tinakhazikitsa pa moyo wathu. Nthawi zina anthufe timadziimba mlandu ngakhale sitinalakwitse chilichonse. Mwachitsanzo, ngati titakhazikitsa mfundo zinazake zovuta kuti tizizitsatira pa moyo wathu, tikhoza kumadziimba mlandu nthawi iliyonse yomwe talephera kuzikwaniritsa. N’chifukwa chake Baibulo limatilimbikitsa kuti tizipewa kudziona kuti ndife olungama kwambiri.—Mlaliki 7:16.
Ndingatani kuti ndisamadziimbe mlandu?
Mukalakwitsa zinazake, ndi bwino kuyesetsa kukonza zomwe mwalakwitsazo m’malo momangokhalira kudziimba mlandu. Kodi mungachite bwanji zimenezi?
Muzivomereza zolakwa zanu. Muzipemphera kwa Yehova a Mulungu kuti akukhululukireni. (Salimo 38:18; Luka 11:4) Mukalapa kuchokera pansi pa mtima komanso mukamayesetsa kupewa kuchitanso tchimolo, mosakayikira Yehova adzayankha pemphero lanu. (2 Mbiri 33:13; Salimo 34:18) Yehova amaona zamumtima mwa munthu, zimene munthu wina aliyense sangathe kuziona. Baibulo limasonyeza kuti Mulungu akaona kuti tikuyesetsa kusiya kuchita zoipa, adzatikhululukira chifukwa iye “ndi wokhulupirika ndiponso wolungama.”—1 Yohane 1:9; Miyambo 28:13.
Komabe ngati mwalakwira munthu wina, mufunika kuvomereza zomwe mwalakwitsazo n’kumupepesa kuchokera pansi pa mtima. Koma kuchita zimenezi si kophweka. Mufunika kukhala wolimba mtima komanso wodzichepetsa. Kupepesa mochokera pansi pa mtima n’kothandiza m’njira ziwiri: kumathandiza kuti inuyo mupepukidwe mumtima, komanso kumathandiza kuti mubwezeretse mtendere.—Mateyu 3:8; 5:23, 24.
Muziganizira malemba ofotokoza zokhudza chifundo cha Mulungu. Mwachitsanzo, taganizirani zimene Baibulo limanena pa 1 Yohane 3:19, 20. Lembali limanena kuti “mitima yathu ingatitsutse,” kutanthauza kuti nthawi zina tikhoza kumadziimba mlandu kwambiri mwinanso n’kumaganiza kuti Mulungu sangatikonde. Komabe, lembali limanenanso kuti “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu.” Zili choncho chifukwa chakuti iye amadziwa chilichonse chokhudza ifeyo, kuphatikizapo mmene timamvera ndiponso zofooka zathu. Iye amadziwanso kuti tinabadwa ndi uchimo womwe umatichititsa kuti tizilakwitsa zinthu. b (Salimo 51:5) Choncho, Mulungu amakhululukira onse amene alapa machimo awo kuchokera pansi pa mtima.—Salimo 32:5.
Musamaganizire kwambiri zolakwa zanu za m’mbuyo. M’Baibulo muli nkhani zambiri za amuna ndi akazi omwe ankachita zinthu zoipa koma pambuyo pake anasintha n’kumachita zabwino. Mmodzi mwa anthu amenewa ndi Saulo wa ku Tariso amene anadzatchedwa mtumwi Paulo. Iye anali Mfarisi ndipo ankazunza kwambiri otsatira a Yesu. (Machitidwe 8:3; 9:1, 2, 11) Koma atazindikira kuti akutsutsana ndi Mulungu komanso Mesiya kapena kuti Khristu, iye analapa n’kusintha moyo wake ndipo anakhala Mkhristu wa chitsanzo chabwino. N’zoona kuti Paulo ankadandaula kwambiri kuti anazunza otsatira a Khristu koma sankangokhalira kuganizira zolakwa zake za m’mbuyo. Kudziwa zoti Mulungu anamusonyeza chifundo chachikulu kunathandiza Paulo kuti akhale mlaliki wakhama ndipo sanasiye kukhulupirira za chiyembekezo cha moyo wosatha.—Afilipi 3:13, 14.
Malemba omwe angakuthandizeni
Salimo 51:17: “Inu Mulungu, simudzanyoza mtima wosweka ndi wophwanyika.”
Zimene lembali limatanthauza: Mulungu sangalephere kukukhululukirani zolakwa zanu ngati mutalapa kuchokera pansi pa mtima. Iye ndi wachifundo.
Miyambo 28:13: “Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino, koma woulula n’kuwasiya adzachitiridwa chifundo.”
Zimene lembali limatanthauza: Ngati titaulula machimo athu kwa Mulungu n’kusintha zochita zathu, iye adzatikhululukira.
Yeremiya 31:34: “Ine ndidzawakhululukira zolakwa zawo ndipo machimo awo sindidzawakumbukiranso.”
Zimene lembali limatanthauza: Mulungu akangotikhululukira satikumbutsanso zolakwa zathu. Iye amatisonyeza chifundo chenicheni.
a Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu.—Ekisodo 6:3.
b Anthufe timalakalaka kuchita zoipa chifukwa tinatengera uchimo kwa kholo lathu Adamu. Iye limodzi ndi mkazi wake Hava, anachimwira Mulungu n’kutaya mwayi wokhala ndi moyo wangwiro ndipo zimenezi zinakhudzanso mbadwa zawo zonse.—Genesis 3:17-19; Aroma 5:12.