Kodi Baibulo Limati Mungasankhe Nokha Zochita Kapena Mulungu Analemberatu Tsogolo Lanu?
Yankho la m’Baibulo
Mulungu sanalemberetu tsogolo lathu, m’malomwake anatilemekeza potipatsa ufulu wosankha. Taonani zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhaniyi.
Mulungu analenga anthu m’chifaniziro chake. (Genesis 1:26) Nyama zimangoyendera nzeru zachibadwa koma ife anthu timafanana ndi Mlengi wathu chifukwa chakuti timatha kusonyeza makhalidwe monga chikondi ndi chilungamo. Mofanananso ndi Mlengi wathu, tili ndi ufulu wosankha.
Zimene timasankha zimakhudza tsogolo lathu. Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tisankhe moyo mwa kumvera mawu a Yehova Mulungu,’ kapena kuti tisankhe kumvera malamulo ake. (Deuteronomo 30:19, 20) Tikanakhala kuti tilibe ufulu wosankha, mawu amenewa akanakhala osamveka ndipo tikananena kuti Mulungu ndi wankhanza kwambiri potiuza zimenezi. M’malo motikakamiza kuchita zimene iye amanena, Mulungu amatichonderera mokoma mtima kuti: “Zingakhale bwino kwambiri mutamvera malamulo anga! Mukatero mtendere wanu udzakhala ngati mtsinje.”—Yesaya 48:18.
Mulungu sanalemberetu kuti zinthu zidzatiyendera bwino kapena ayi. Ngati tikufuna kuti zinthu zitiyendere bwino tiyenera kuchita khama. Paja Baibulo limati: “Chilichonse chimene dzanja lako lapeza kuti lichite, uchichite ndi mphamvu zako zonse.” (Mlaliki 9:10) Limanenanso kuti: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira.”—Miyambo 21:5.
Chifukwa cha mphatso ya ufulu wosankha imene Mulungu anatipatsa, timatha kumukonda ndi ‘mtima wathu wonse’ mwa kufuna kwathu.—Mateyu 22:37.
Kodi Mulungu amagwiritsa ntchito mphamvu zake pa zinthu zonse?
Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu ndi Wamphamvuyonse ndipo mphamvu zake ndi zopanda malire. (Yobu 37:23; Yesaya 40:26) Koma sikuti amagwiritsa ntchito mphamvu zakezo pa zinthu zonse. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti Mulungu ‘anadziletsa’ pochita zinthu ndi Ababulo, omwe anali adani a anthu ake. (Yesaya 42:14) Masiku anonso, iye amadziletsa pochita zinthu ndi anthu amene amazuna anzawo pogwiritsa ntchito molakwika ufulu wawo wosankha. Koma sikuti adzangowalekerera mpaka kalekale.—Salimo 37:10, 11.