Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Banja?

Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Banja?

Yankho la m’Baibulo

 Mulungu atalenga mwamuna ndi mkazi woyambirira, anakonza zoti akhale banja. Iye anakhazikitsa banja kuti likhale mgwirizano wapadera pakati pa mwamuna ndi mkazi komanso kuti likhale malo abwino olereramo ana.​—Genesis 1:27, 28; 2:18.

 Mulungu amafuna kuti mwamuna ndi mkazi wake azikhala mosangalala. (Miyambo 5:18) Mulungu anakhazikitsa mfundo zokhudza banja komanso zomwe zingathandize kuti banjalo liziyenda bwino. Mfundozi zimapezeka m’Baibulo.

Zomwe zili munkhaniyi

 Kodi Mulungu anakhazikitsa mfundo zotani zokhudza banja?

 Kuyambira pachiyambi, Mulungu anakonza zoti m’banja muzikhala mwamuna ndi mkazi mmodzi. (Genesis 2:24) Mulungu savomereza mitala, kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha kapenanso zoti mwamuna ndi mkazi osakwatirana azikhala limodzi. (1 Atesalonika 4:3) Yesu analimbikitsa otsatira ake kuti azilemekeza mfundo zokhudza banja zomwe Mulungu anakhazikitsa.​—Maliko 10:6-8.

 Mulungu amaona kuti banja ndi mgwirizano wa moyo wonse. Mwamuna ndi mkazi akamakwatirana, aliyense amalonjeza kuti adzakhala wokhulupirika kwa mnzake komanso kuti azidzakhala limodzi kwa nthawi yonse yomwe adzakhale ndi moyo. Mulungu amafuna kuti anthu okwatirana azisunga lonjezo limeneli.​—Maliko 10:9.

 Kodi Mulungu amalola kuti anthu okwatirana azipatukana kapena kusudzulana?

 Nthawi zina mwamuna ndi mkazi wake akhoza kusiyana kwa kanthawi mwina chifukwa chakuti wina akufunika kukathandiza makolo kapena wachibale pakagwa mavuto amwadzidzidzi. Komabe, Baibulo silivomereza kuti anthu azipatukana chifukwa cha mavuto am’banja. M’malomwake, limalimbikitsa anthu okwatiranawo kuti azikambirana akasemphana maganizo.​—1 Akorinto 7:10.

 Malemba amavomereza kuti anthu okwatirana akhoza kusudzulana kapena kuthetsa banja lawo ngati wina wachita chigololo. (Mateyu 19:9) Choncho mogwirizana ndi zomwe Malemba amanena, ngati mwamuna ndi mkazi atapatukana kapena kusudzulana pa zifukwa zina, osati chifukwa cha chigololo, zingakhale zosavomerezeka kuti mwamuna kapena mkaziyo akhale pachibwenzi kapena kukwatirananso ndi munthu wina.​—Mateyu 5:32; 1 Akorinto 7:11.

 Kodi Mulungu amafuna kuti okwatirana akalembetse kaye kuboma kuti banja lawo likhale lovomerezeka?

 Mulungu amafuna kuti tizimvera malamulo omwe boma linakhazikitsa pa nkhani yokhudza banja. (Tito 3:1) Mwamuna ndi mkazi akalembetsa banja lawo mogwirizana ndi malamulo, amasonyeza kuti amalemekeza akuluakulu a boma komanso mfundo za Mulungu zomwe zimati banja ndi mgwirizano wa moyo wonse. a

 Kodi Baibulo limati mwamuna ndi mkazi ali ndi udindo wotani m’banja?

  •   Ali ndi udindo wothandizana. Mwamuna ndi mkazi wake ayenera kukondana ndi kulemekezana. (Aefeso 5:33) Munthu amene ali pabanja ayenera kugonana ndi mkazi kapena mwamuna wake yekha ndipo ayenera kupewa kuchita zinthu zilizonse zosakhulupirika. (1 Akorinto 7:3; Aheberi 13:4) Ngati ali ndi ana, ayenera kuthandizana polera anawo.​—Miyambo 6:20.

     Baibulo silinena chilichonse pa nkhani ya amene angamagwire ntchito yolembedwa kapenanso ntchito zapakhomo. Okwatiranawo ayenera kukambirana mogwirizana ndi zomwe zingakhale zothandiza pa banja lawo.

  •   Udindo wa mwamuna. Baibulo limanena kuti “mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake.” (Aefeso 5:23) Mwamuna ndi mutu m’njira yakuti, iye ndi amene ali ndi udindo wotsogolera banja lake komanso wosankha zinthu zomwe zingathandize mkazi ndi ana.

     Iye ayenera kuonetsetsa kuti mkazi ndi ana ake ali ndi zonse zofunikira kuti akhale athanzi, osangalala komanso kuti akhale pa ubwenzi ndi Mulungu. (1 Timoteyo 5:8) Mwamuna ayenera kusonyeza kuti amayamikira zomwe mkazi wake amachita komanso makhalidwe ake abwino. Angachite zimenezi akamachita zinthu mogwirizana ndi mkazi wake pomumvetsera akamanena maganizo ake komanso akamamufunsa maganizo ake asanasankhe zochita. (Miyambo 31:11, 28) Baibulo limati mwamuna, ayenera kuchita zinthu mwachikondi akamasamalira banja lake.​—Akolose 3:19.

  •   Udindo wa mkazi. Baibulo limanena kuti “mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.” (Aefeso 5:33) Mulungu amasangalala kwambiri mkazi akamalemekeza udindo umene mwamuna wake anapatsidwa ndi Mulungu.

     Mkazi ali ndi udindo wothandiza mwamuna wake akamasankha zochita komanso ayenera kumuthandiza kuti akwaniritse udindo wake monga mutu. (Genesis 2:18) Baibulo limanena kuti mkazi amene amakwaniritsa udindo wake m’banja ndi wamtengo wapatali.​—Miyambo 31:10.

 Kodi Mulungu amafuna kuti mabanja amasiku ano azikhala ndi ana?

 Ayi. Kalelo, Mulungu analamula atumiki ake ena kuti akhale ndi ana. (Genesis 1:28; 9:1) Koma lamuloli silikhudza Akhristu. Nayenso Yesu sanalamule otsatira ake kuti azikhala ndi ana. Ngakhalenso ophunzira a Yesu sananenepo kuti anthu akakwatirana ayenera kukhala ndi ana. Mwamuna ndi mkazi wake ayenera kusankha okha ngati akufuna kukhala ndi ana kapena ayi.

 Kodi Baibulo lingathandize bwanji banja langa?

 M’Baibulo muli mfundo zomwe zingathandize anthu okwatirana kuti akhale ndi banja labwino. Mfundo za m’Baibulo zingathandize mwamuna ndi mkazi wake kuti apewe kapenanso kuthetsa mavuto am’banja lawo.

 Mfundo za m’Baibulo zingathandize mwamuna ndi mkazi wake kuti . . .

a Kuti mudziwe zomwe Baibulo limanena pa nkhani ya ukwati wachikhalidwe kapena wolembetsa ku boma, onani Nsanja ya Olonda ya October 15, 2006, tsamba 21, ndime 12.