Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Afilipi 4:6, 7​—“Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse”

Afilipi 4:6, 7​—“Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse”

 “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.”​—Afilipi 4:6, 7, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Musadere nkhawa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.”​—Afilipi 4:6, 7, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Afilipi 4:6, 7

 Anthu amene amalambira Mulungu angachepetse nkhawa zawo akamapemphera kwa iye. Mulungu amalonjeza kuti adzawapatsa mtendere umene ungawathandize kuti asamade nkhawa kwambiri komanso udzateteza maganizo ndi mtima wawo. Vesi 6 limafotokoza mitundu ina ya pemphero imene ingawathandize kupeza mtendere umenewu.

 Pembedzero ndi kupemphera mochonderera kwambiri. Munthu akhoza kuchonderera Mulungu, kapena kuti kupembedza, akakhala pa mavuto aakulu kwambiri ngati mmene zinalili ndi Yesu. (Aheberi 5:7) Nthawi zambiri munthu amapereka mapemphero oterewa mobwerezabwereza.

 Zopempha ndi zinthu zonse zimene mungapemphe kwa Mulungu. Anthu a Mulungu angamupemphe kuti awathandize “pa chilichonse” chimene angakumane nacho. Koma mapempherowa ayenera kukhala ogwirizana ndi zimene Baibulo limanena kuti Mulungu amafuna.​—1 Yohane 5:14.

 Mapemphero a chiyamiko ndi othokoza Mulungu chifukwa cha zimene watichitira komanso zimene adzatichitire m’tsogolo. Tikamaganizira zinthu zimene tingathokoze nazo Mulungu, m’pamene tingakhale osangalala.​—1 Atesalonika 5:16-18.

 Anthu olambira Mulungu akamapereka mapemphero amitundu imeneyi, iye amawapatsa mtendere. “Mtendere wa Mulungu” ndi mtendere wamumtima umene tingakhale nawo chifukwa chokhala naye pa ubwenzi wolimba. (Aroma 15:13; Afilipi 4:9) Mtenderewu “umaposa kuganiza mozama kulikonse” chifukwa umachokera kwa Mulungu komanso ungatithandize m’njira zimene sitingayembekezere.

 Vesili limanena kuti mtendere wa Mulungu ungateteze mitima yathu. Mawu a Chigiriki amene anamasuliridwa kuti ‘kuteteza’ amafanana ndi mawu amene amanena za zimene asilikali ankachita poteteza mzinda. Mofanana ndi zimenezi, mtendere wa Mulungu umateteza mtima ndi maganizo a munthu. Umamuthandiza kuti asamapanikizike ndi mavuto amene amakumana nawo.

 Mtendere umene Mulungu amatipatsa umatiteteza “mwa Khristu Yesu.” Zili choncho chifukwa tingakhale pa ubwenzi ndi Mulungu chifukwa cha Yesuyo. Paja iye anapereka moyo wake nsembe chifukwa cha machimo athu. Ndiye tikamamukhulupirira, Mulungu adzatidalitsa. (Aheberi 11:6) Komanso tiyenera kudzera mwa Yesu popemphera kwa Mulungu. Iye ananena kuti: “Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.”​—Yohane 14:6; 16:23.

Nkhani Yonse ya Afilipi 4:6, 7

 Buku la m’Baibulo la Afilipi ndi kalata imene mtumwi Paulo analembera Akhristu okhala mumzinda wa Filipi. a M’mavesi amene panopa ali m’chaputala 4, Paulo analimbikitsa anthu amumpingowo kuti azisangalala ndipo anawathokoza chifukwa chokhala ndi mtima wopatsa, zomwe zinamusangalatsa. (Afilipi 4:4, 10, 18) Iye anafotokoza mmene pemphero lingawathandizire kuti apeze mtendere wa Mulungu. Anawauzanso zinthu zabwino zimene angaganize komanso kuchita zomwe zingachititse kuti “Mulungu wamtendere” aziwathandiza.​—Afilipi 4:8, 9.

a Umapezeka masiku ano m’dziko la Greece.