KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO
Genesis 1:1—“Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi”
“Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.”—Genesis 1:1, Baibulo la Dziko Latsopano.
“Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.”—Genesis 1:1, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.
Tanthauzo la Genesis 1:1
Mawu oyamba a m’Baibulowa amanena mfundo ziwiri zoona zomwe n’zofunika. Choyamba, amanena kuti “kumwamba ndi dziko lapansi,” kapena kuti zinthu zonse zooneka ndi maso m’chilengedwe, zinali ndi chiyambi. Chachiwiri, zonsezi zinalengedwa ndi Mulungu.—Chivumbulutso 4:11.
Baibulo silinena nthawi kapena njira imene Mulungu analengera zinthuzi. Koma limanena kuti analenga zinthuzi pogwiritsa ntchito ‘mphamvu zake zochuluka komanso zoopsa, ndiponso . . . mphamvu [zake] zambiri zochitira zinthu.’—Yesaya 40:26.
Mawu oti “kulenga” anamasuliridwa kuchokera ku mawu a Chiheberi amene amagwiritsidwa ntchito ponena za zinthu zimene Mulungu yekha amachita. a Ndipotu m’Baibulo Yehova b Mulungu yekha ndi amene amatchulidwa kuti Mlengi.—Yesaya 42:5; 45:18.
Nkhani yonse ya Genesis 1:1Genesis 1:1
Vesi loyamba la m’Baibuloli ndi mawu oyamba a nkhani yofotokoza za kulengedwa kwa zinthu mu Genesis chaputala 1 ndi 2. Kuyambira pa Genesis 1:1 mpaka 2:4, Baibulo limafotokoza mwachidule zimene Mulungu anachita polenga dziko lapansi ndi zinthu zonse zapadzikoli, kuphatikizapo mwamuna ndi mkazi oyamba. Baibulo litafotokoza mwachidule zimenezi, limafotokoza mwatsatanetsatane kulengedwa kwa mwamuna ndi mkazi.—Genesis 2:7-25.
Buku la Genesis limafotokoza kuti Mulungu analenga zinthu pa “masiku” 6. Masiku amenewa sanali a maola 24 koma a nthawi yosadziwika. Sikuti mawu oti “tsiku” nthawi zonse amanena za maola 24 basi. Mwachitsanzo, lemba la Genesis 2:4 limagwiritsa ntchito mawu oti “tsiku” kutanthauza “nthawi.” Limanena za ‘tsiku’ limene Mulungu anapanga zinthu zonse zimene anazilenga m’masiku 6.
Maganizo Olakwika Okhudza Genesis 1:1
Maganizo olakwika: Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi zaka masauzande angapo zapitazo.
Zoona zake: Baibulo silinena nthawi imene zinthuzi zinalengedwa. Mawu a pa Genesis 1:1 sasemphana ndi zimene asayansi amanena kuti kumwamba ndi dziko lapansi zakhalapo kwa zaka mabiliyoni angapo. c
Maganizo olakwika: Lemba la Genesis 1:1 limasonyeza kuti Mulungu ndi Utatu, kapena kuti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi chifukwa mawu a Chiheberi amene anamasuliridwa kuti “Mulungu” m’vesili sanena za Mulungu mmodzi yekha.
Zoona zake: Mawu oti “Mulungu” anamasuliridwa kuchokera ku mawu a Chiheberi akuti ’Elo·himʹ, omwe sanena za mmodzi yekha chifukwa amasonyeza ukulu kapena kulemekezeka. Buku lina lofotokoza mawu a m’Baibulo amanena kuti mawu oti ’Elo·himʹ omwe anagwiritsidwa ntchito pa Genesis 1:1 “nthawi zonse amakhala ndi verebu yonena za munthu mmodzi kusonyeza kuti mawuwo sakunena za milungu ingapo koma ndi olemekeza basi.—New Catholic Encyclopedia, Second Edition, Voliyumu 6, tsamba 272.
Werengani Genesis chaputala 1, mawu am’munsi ndi malifalensi ake.
a Ponena za mawu amenewa, Baibulo lina lophunzirira limati: “Verebu ya Chiheberi yakuti bara’, yotanthauza kuti ‘kulenga,’ sigwiritsidwa ntchito pofotokoza zimene munthu akuchita. Choncho mawuwa amanena za ntchito imene Mulungu yekha amagwira.”—HCSB Study Bible, tsamba 7.
b Yehova ndi dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.
c Ponena za mawu a Chiheberi amene anamasuliridwa kuti “pa chiyambi,” buku lina lofotokoza Baibulo limati: “Mawuwa sasonyeza kuti nthawiyo inali yaitali bwanji.”—The Expositor’s Bible Commentary, Revised Edition, Voliyumu 1, tsamba 51.