Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Maliko 1:15​—“Ufumu wa Mulungu Wayandikira”

Maliko 1:15​—“Ufumu wa Mulungu Wayandikira”

 “Nthawi yoikidwiratu yakwaniritsidwa! Ufumu wa Mulungu wayandikira! Lapani anthu inu! Khulupirirani uthenga wabwino!”​—Maliko 1:15, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Nthawi yakwanira, ndipo Ufumu wa Mulungu wayandikira; tembenukani mtima, khulupirirani uthenga wabwino.”​—Maliko 1:15, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Maliko 1:15

 Yesu Khristu ananena kuti Ufumu wa Mulungu a “wayandikira” chifukwa choti iye anali Mfumu yam’tsogolo ya Ufumuwo ndipo analipo pa nthawiyo.

 Yesu sankatanthauza kuti Ufumuwo unali utayamba kale kulamulira. Nthawi ina polankhula ndi ophunzira ake, anasonyeza kuti Ufumu unali usanabwere. (Machitidwe 1:6, 7) Koma Yesu anali atabwera pa nthawi yoikidwiratu, m’chaka chimene Baibulo linaneneratu kuti adzafike monga Mfumu yam’tsogolo. b N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Nthawi yoikidwiratu yakwaniritsidwa.” Ankatanthauza kuti nthawi yoti iye ayambe ntchito yake yolalikira uthenga wabwino wokhudza Ufumu.​—Luka 4:16-21, 43.

 Kuti anthu athandizidwe ndi uthenga wabwino, ankafunika kulapa, kapena kuti kunong’oneza bondo chifukwa cha machimo awo akale n’kuyamba kutsatira mfundo za Mulungu. Anthu amene analapa anasonyeza kuti ankakhulupirira uthenga wabwino wokhudza Ufumu wam’tsogolowo.

Nkhani yonse ya Maliko 1:15

 Yesu ananena mawuwa atangoyamba utumiki wake ku Galileya. Lemba la Mateyu 4:17, lomwe likufotokoza nkhani yomweyi, limanena kuti “Kuyambira nthawi imeneyo,” Yesu ankalalikira za Ufumu wa Mulungu. Nkhani yaikulu imene Yesu ankalalikira kapena kuphunzitsa inali yokhudza Ufumu. Mabuku 4 a Uthenga Wabwino c amatchula Ufumu nthawi zoposa 100, makamaka pa mawu amene Yesu ananena. Mawu a Yesu amene amapezeka m’Baibulo amanena za Ufumu wa Mulungu kuposa nkhani ina iliyonse.

Werengani Maliko chaputala 1, mawu am’munsi ndi malifalensi ake.

a Ufumu wa Mulungu ndi boma lakumwamba lomwe Mulungu wakhazikitsa n’cholinga choti lichite zimene iye akufuna padzikoli. (Danieli 2:44; Mateyu 6:10) Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani yakuti “Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

b Yesu ankafunika kukhala mfumu kuti akwaniritse udindo wake wokhala Mesiya amene ananenedweratu, kapena kuti munthu wapadera woimira Mulungu. Kuti mudziwe zambiri zokhudza maulosi a m’Baibulo osonyeza kuti Yesu anali Mesiya, onani nkhani yakuti “Kodi Maulosi Onena za Mesiya Amatsimikizira Kuti Yesu Analidi Mesiya?”

c Mabuku a Uthenga Wabwino ndi mabuku 4 oyambirira a m’Malemba Achigiriki, omwe anthu ambiri amati Chipangano Chatsopano. Mabukuwa amafotokoza moyo ndi utumiki wa Yesu.