1 AKORINTO 7-9
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU |Umbeta ni Mphatso
7:32, 35, 38
Kwa zaka zambili, Akhristu ambili amakamba kuti kukhala mbeta kuli na maubwino apadela. Kumawathandiza kuwonjezela utumiki, kupeza mabwenzi osiyana-siyana, komanso kuyandikila kwambili Yehova.
ZOFUNIKA KUSINKHA-SINKHA: Ngati ndinu mbeta, mungacite ciani kuti umbeta wanu ukhale waphindu?
Kodi anthu mu mpingo angacite ciani kuti alimbikitse na kuthandiza aja amene ni mbeta?