1 AKORINTO 14-16
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU |Mulungu Adzakhala “Zinthu Zonse kwa Aliyense”
15:24-28
Anthu okhulupilika kwa Yehova ayembekezela kudzakhala na tsogolo labwino. Tikamauzako ena mogwila mtima za ciyembekezo cathu, ciyembekezoco cimakhomelezeka mwa ife. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti aziganizila nthawi ya kumapeto kwa Ulamulilo wa Khristu wa Zaka 1000, pamene Yehova adzakhala “zinthu zonse kwa aliyense.”
Ni madalitso ati amene muyembekezela mwacidwi kudzayaona? Nanga n’cifukwa ciani?
N’ciani cimakutsimikizilani kuti malonjezo a Mulungu adzakwanilitsidwa?