UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Khalani na Colinga Cocita Maphunzilo Aumulungu
CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Mlangizi Wamkulu Yehova, amatipatsa maphunzilo abwino koposa. Kwaulele, iye amatiphunzitsa mmene tingakhalile na umoyo wabwino, ndiponso amatikonzekeletsa mmene tingakhalile na tsogolo labwino. (Yes. 11:6-9; 30:20, 21; Chiv. 22:17) Kupitila m’maphunzilo aumulungu, Yehova amatiphunzitsa mmene tingauzileko ena uthenga wopatsa moyo.—2 Akor. 3:5.
MMENE TINGACITILE:
-
Kulitsani khalidwe la kudzicepetsa na kufatsa.—Sal. 25:8, 9
-
Landilani maphunzilo amene Yehova akukupatsani pali pano. Mwacitsanzo mbali za m’sukulu pa msonkhano wa mkati mwa wiki
-
Dziikileni zolinga zauzimu.—Afil. 3:13
-
Yesetsani kudzipeleka kuti muyenelele kucita maphunzilo owonjezeleka.—Afil. 3:8
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI OLEMELA MWAUZIMU CIFUKWA COPHUNZITSIDWA NA YEHOVA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:
-
Ni zopinga zotani zimene ofalitsa ena anakumana nazo kuti angene Sukulu ya Alengezi a Ufumu?
-
Kodi Sukulu ya Alengezi a Ufumu imaphunzitsa zotani?
-
Kodi abale na alongo amene anatsiliza maphunzilo a Sukulu ya Alengezi a Ufumu anathandizidwa bwanji na abale a m’mipingo imene anatumizidwako?
-
Kodi cofunika n’ciani kuti munthu ayenelele kungena Sukulu ya Alengezi a Ufumu? (kr 189)
-
Ni maphunzilo ena ati amene mungaciteko m’gulu la Yehova?