UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kodi Mudzakonzekela Bwanji Cikumbutso?
Kuyambila caka cino, tidzayamba kukhala na nthawi yoculuka yokonzekela Cikumbutso ca imfa ya Khristu. Ngati Cikumbutso cacitika mkati mwa wiki, Msonkhano wa Umoyo na Utumiki, suzikhalako. Komanso, nkhani ya anthu onse na Phunzilo la Nsanja ya Mlonda, kuzikhala kulibe ngati Cikumbutso cacitika pa wikendi. Kodi mudzaseŵenzetsa nthawi imeneyi mwanzelu pokonzekela Cikumbutso? Monga mmene zinalili m’nthawi ya atumwi, makonzedwe afunika kupangidwa okhudza cocitika capadelaci. (Luka 22:7-13; km 3/15 1) Koma tonsefe tifunika kukonzekeletsa mitima yathu. Tingacite bwanji zimenezi?
-
Ganizilani ubwino wopezekapo.—1 Akor. 11:23-26
-
Pemphelani na kuganizila mmene ubwenzi wanu ulili na Yehova.—1 Akor. 11:27-29; 2 Akor. 13:5
-
Ŵelengani na kusinkha-sinkha Malemba amene akamba za tanthauzo la Cikumbutso.—Yoh. 3:16; 15:13
Ofalitsa ena amaŵelenga na kusinkha-sinkha Malemba a pa nyengo ya Cikumbutso opezeka m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku. Ena amaŵelenga Malemba amene ali pa chati imene ili pansipa. Enanso amaŵelenga nkhani za m’maganizini a Nsanja ya Mlonda zokamba za Cikumbutso na cikondi cimene Yehova na Yesu anatisonyeza. Njila iliyonse imene mungasankhe, idzakuthandizani kuyandikila kwambili Yehova na Mwana wake.