February 15- 21
NEHEMIYA 9–11
Nyimbo 84 ndi Pemphelo
Mau Oyamba (Mph. 3 kapena zocepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Olambila Okhulupilika Amacilikiza Dongosolo la Gulu la Mulungu”: (Mph. 10)
Neh. 10:28-30—Anavomela kuti sadzakwatilana ndi ‘anthu a m’dzikolo’ (w98 10/15 tsa. 21 ndime 11)
Neh. 10:32-39—Iwo anavomeleza kucilikiza kulambila koona m’njila zosiyanasiyana (w98 10/15 tsa. 21 ndime 11-12)
Neh. 11:1, 2—Iwo anacilikiza dongosolo la gulu la Mulungu ndi mtima wonse (w06 2/1 tsa. 11 ndime 6; w98 10/15 tsa. 22 ndime 13)
Kufufuza Cuma Cakuuzimu: (Mph. 8)
Neh. 9:19-21—Kodi Yehova waonetsa bwanji kuti amasamalila bwino kwambili anthu ake? (w13 9/1 tsa. 9 ndime 9-10)
Neh. 9:6-38—Ndi citsanzo cabwino citi cimene Alevi anatipatsa pa nkhani ya pemphelo? (w13 10/1 tsa. 20-21 ndime 6-7)
Kodi kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kundiphunzitsa ciani za Yehova?
Ndi mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingagwilitsile nchito mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibulo: Neh. 11:15-36 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
KUONJEZELA LUSO LANU MU ULALIKI
Ulendo Woyamba: (Mph. 2 kapena zocepelapo) Gaŵilani magazini a Galamukani! yatsopano mwakugwilitsila nchito nkhani ya mutu wakuti “Mfundo Zothandiza Mabanja—Kodi Mungatani Kuti Mukhale ndi Anzanu Apamtima?” Ndiyeno yalani maziko a ulendo wobwelelako.
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Citani citsanzo coonetsa wofalitsa akucita ulendo wobwelelako kwa munthu amene anaonetsa cidwi pa nkhani ya mutu wakuti “Mfundo Zothandiza Mabanja—Kodi Mungatani Kuti Mukhale ndi Anzanu Apamtima?” yopezeka mu Galamukani! yatsopano, ndipo ayale maziko a ulendo wotsatila.
Phunzilo la Baibulo: (Mph. 6 kapena zocepelapo) Citani citsanzo coonetsa mmene mungayambitsile phunzilo la Baibulo. (bh tsa. 32-33 ndime 13-14)
UMOYO WATHU WACIKRISTU
“Umoyo Wabwino Koposa” (“The Best Life Ever”): (Mph. 15) Nkhani yokambilana. Yambani ndi kuonetsa vidiyo imeneyi. Kenako, kambilanani mafunso amene ali m’nkhani ino. Funsani wofalitsa amene sali pa banja kapena yemwe anatumikila Yehova kwa zaka zambili asanaloŵe m’banja. (1 Akor. 7:35) Nanga adalitsidwa bwanji cifukwa ca cakutelo?
Phunzilo la Baibulo la Mpingo: ia Mutu 9 ndime 1-13 (Mph. 30)
Bwelezani Mfundo Zimene Taphunzila Komanso Fotokozani Zomwe Tidzaphunzila Mlungu Wotsatila (Mph. 3)
Nyimbo 76 ndi Pemphelo