UMOYO WACIKHIRISTU
“Inu Mulungu Wanga, Cikhulupililo Canga Cili mwa Inu”
Tifunika kudalila Yehova kwambili pamene zinthu zikuyenda bwino ndi pa nthawi yovuta. (Sal. 25:1, 2) M’zaka za m’ma 700 B.C.E., Ayuda ku Yudeya anakumana ndi vuto imene inayesa cikhulupililo cawo mwa Mulungu. Tingaphunzile zambili pa zimene zinacitika. (Aroma 15:4) Mukatamba vidiyo yakuti, “Inu Mulungu Wanga, Cikhulupililo Canga Cili mwa Inu” yankhani mafunso aya.
-
Kodi Hezekiya anakumana ndi cothetsa nzelu canji?
-
Kodi Hezekiya anaseŵenzetsa bwanji mfundo ya pa Miyambo 22:3 atadziŵa kuti adani akubwela kudzazinga mzinda wawo?
-
N’cifukwa ciani Hezekiya anakanilatu zodzipeleka kwa Asuri, kapena kupanga mgwilizano ndi Aiguputo?
-
Kodi Hezekiya ni citsanzo cabwino motani kwa Akhiristu?
-
N’zocitika ziti zimene zingatiyese pa cidalilo cathu mwa Yehova?