January 23-29
YESAYA 38-42
Nyimbo 78 ena Pemphelo
Mau Oyamba (3 min. kapena zocepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Yehova Amapeleka Mphamvu kwa Munthu Wotopa”: (10 min.)
Yes. 40:25, 26—Yehova ndiye Gwelo la mphamvu zonse (ip-1 409-410 pala. 23-25)
Yes. 40:27, 28—Yehova amaona mavuto na zinthu zopanda cilungamo zimene zimaticitikila (ip-1 413 pala. 27)
Yes. 40:29-31—Yehova amapeleka mphamvu kwa onse omudalila (ip-1 413-415 pala. 29-31)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Yes. 38:17—Kodi Yehova amaponya bwanji macimo athu onse kumbuyo kwake? (w03 7/1 peji 17 pala. 17)
Yes. 42:3—Kodi ulosiwu unakwanilitsika bwanji pa Yesu? (w15 2/15 peji 8 pala. 13)
Kodi ine pacanga, kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno kwaniphunzitsa ciani za Yehova?
Ni mfundo ziti pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno zimene ine pacanga ningaseŵenzetse mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. kapena zocepelapo) Yes. 40:6-17
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 min. kapena zocepelapo) fg—Kambilanani funso 1, pala. 1 m’phunzilo 8, ndipo yalani maziko a ulendo wobwelelako.
Ulendo Wobwelelako: (4 min. kapena zocepelapo) fg—Citani ulendo wobwelelako kwa munthu amene analandila kabuku ka Uthenga Wabwino mwa kupitiliza phunzilo 8.
Phunzilo la Baibo: (6 min. kapena zocepelapo) lv peji 38-39 pala. 6-7—Onetsani mmene tingam’fikile pamtima munthu.
UMOYO WATHU WACIKHIRISTU
“Tizikumbukila Kupemphelela Akhiristu Anzathu Amene Akuzunziwa”: (15 min.) Kukambilana. Yambani mwa kutambitsa vidiyo yakuti Mlandu wa Mboni za Yehova Ulowanso mu Khoti ku Taganrog—Kodi Cilungamo Cidzacitika Liti? (Yendani ku mavidiyo pa GULU).
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr nkhani 7 pala. 10-18, na kabokosi papeji 73
Kubwelelamo na Kuchulako za Mlungu Wotsatila (3 min.)
Nyimbo 9 na Pemphelo