Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Tetezani Cikwati Canu

Tetezani Cikwati Canu

Yehova amaona kuti malumbilo a cikwati ni nkhani yaikulu. Iye anakamba kuti mwamuna na mkazi wake afunika kukhala limodzi osalekana. (Mat. 19:5, 6) Pakati pa anthu a Mulungu pali ambili amene ali na vikwati vabwino. Ngakhale n’conco, kulibe cikwati cangwilo. Banja lililonse limakumana na mavuto. Conco tiyenela kupewa maganizo amene anthu ambili m’dzikoli ali nawo akuti kupatukana na kusudzulana ndiwo mankhwala othetsela mavuto m’cikwati. Kodi mabanja acikhristu angateteze bwanji cikwati cawo?

Onani mfundo zisanu izi zofunika.

  1. Tetezani mtima wanu mwa kupewa zinthu monga kuceza mokopana komanso zosangalatsa zolimbikitsa ciwelewele zimene zingathe kusokoneza cikwati.—Mat. 5:28; 2 Pet. 2:14.

  2. Limbitsani ubwenzi wanu na Mulungu, ndipo kulitsani mtima wofuna kum’kondweletsa m’cikwati canu.—Sal. 97:10.

  3. Pitilizani kuvala umunthu watsopano, ndipo muzicitila mnzanu wa m’cikwati ngakhale zinthu zocepa cabe zoonetsa kukoma mtima kuti mum’kondweletse.—Akol. 3:8-10, 12-14.

  4. Muzikambilana mwaulemu na moona mtima. —Akol. 4:6.

  5. Muzipeleka mangawa a m’ciwati mwacikondi. —1 Akor. 7:3, 4; 10:24.

Akhristu akamalemekeza cikwati, ndiye kuti akulemekeza Yehova amene ni Woyambitsa cikwati.

ONETSANI VIDIYO YAKUTI TIFUNIKA ‘KUTHAMANGA MOPILILA’—TSATILANI MALANGIZO A MPIKISANO, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Ngakhale kuti cikwati cingakhale na ciyambi cabwino, ni mavuto ati amene angabuke?

  • Kodi mfundo za m’Baibo zingawathandize bwanji anthu amene amaona kuti sakondedwa m’cikwati?

  • Seŵenzetsani mfundo za m’Baibo kuti mukhale acimwemwe m’cikwati canu

    Kodi Yehova anaika malamulo otani m’cikwati?

  • Kuti cikwati ciziyenda bwino, kodi mwamuna na mkazi wake ayenela kucita ciani?