UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Acinyamata—Auzeni za Mumtima Mwanu Makolo Anu
N’cifukwa ciani muyenela kumasuka kuuza makolo anu za mumtima mwanu? (Miy. 23:26) Cifukwa Yehova anawapatsa udindo wokusamalilani na kukutsogolelani. (Sal. 127:3, 4) Cingakhale covuta kwa iwo kukuthandizani ngati simuwafotokozela nkhawa zanu zonse. Komanso mungataye mwayi wopindula na nzelu zimene apeza pa umoyo wawo. Koma kodi n’kulakwa kusawafotokozelako zina zimene mukuganiza? Osati kwenikweni—malinga ngati simukucita zinthu zaciphamaso.—Miy. 3:32.
Kodi mungakambe nawo bwanji makolo anu? Yesani kupeza nthawi yabwino kwa inu na iwo. Ngati zimenezo n’zovuta, mungalembele kalata mmodzi wa makolo anu yowauzako za mumtima mwanu. Nanga bwanji ngati afuna kuti mukambilane nawo nkhani imene inu sindinu omasuka kuikambilana? Kumbukilani kuti iwo amafunitsitsa kukuthandizani. Muziwaona kuti ni mabwenzi anu, osati adani anu. Ngati muyesetsa kukambilana momasuka na makolo anu, mudzapindula kwa moyo wanu wonse, inde kwamuyaya.—Miy. 4:10-12.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI UMOYO WANGA NILI WACICEPELE—KODI NINGAKAMBE NAWO BWANJI MAKOLO ANGA? KENAKO KAMBILANANI MAFUNSO AWA:
-
Kodi Esther na Partik anazindikila ciani zokhudza umoyo wawo?
-
Mungaphunzile ciani pa citsanzo ca Yesu?
-
Kodi makolo anu aonetsa bwanji kuti amakukondani?
-
Ni mfundo za m’Baibo ziti zimene zingakuthandizeni kuti muzikambilana na makolo anu?