January 17-23
OWERUZA 20-21
Nyimbo 47 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Pitilizani Kupempha Citsogozo ca Yehova”: (Mph. 10)
Kufufuza Cuma Cauzimu: (Mph. 10)
Ower. 20:16—Kodi gulaye anali kumugwilitsila nchito bwanji pankhondo m’nthawi yakale? (w14 5/1 31 ¶4-6)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4) Ower. 20:1-13 (th phunzilo 10)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (Mph. 3) Mukayamba na makambilano acitsanzo, mwininyumba akambe mawu ofala kwanuko ofuna kukanila ulaliki, koma mwaluso loŵelani pa mawu amenewo. (th phunzilo 5)
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4) Yambani na makambilano acitsanzo. Chulani za vidiyo yakuti Mboni za Yehova—Kodi Ndife Anthu Otani? (koma musaitambitse) (th phunzilo 17)
Phunzilo la Baibo: (Mph. 5) lffi phunzilo 03 ndime yoyamba na mfundo 1-3 (th phunzilo 4)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Zacilengedwe Zimatilimbikitsa Kudalila Kwambili Nzelu za Yehova”: (Mph. 15) Kukambilana. Onetsani vidiyo ya Chichewa yakuti Kodi Zinangocitika Zokha? Mmene Nyerere Zimapewera Kutchingirana Njira komanso yakuti Kodi Zinangochitika Zokha? Mmene Njuchi Imaulukira. Limbikitsani omvetsela kuti azikambilana nkhani za pa jw.org zakuti “Kodi Zinangochitika Zokha?” na mavidiyo ake pa kulambila kwawo kwa pabanja.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30) lfb phunzilo 73
Mawu Othela (Mph. 3)
Nyimbo 66 na Pemphelo