UMOYO NA UTUMIKI WATHU–KABUKU KA MISONKHANO June 2018
Makambilano Acitsanzo
Makambilano acitsanzo okhudza maulosi a m’Baibo na masiku otsiliza.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Kukwanilitsidwa kwa Maulosi Okhudza Yesu
Gwilizanitsani cocitika mu umoyo wa Yesu na ulosi umene cocitikaco cinakwanilitsa.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Tsatilani Mapazi a Khristu Mosamala Kwambili
Yesu anapeleka citsanzo cimene tiyenela kutengela, maka-maka ngati tikuyesedwa kapena kuzunzidwa.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Tengelani Kudzicepetsa kwa Mariya
Yehova Mulungu anapatsa Mariya mwayi wapadela cifukwa anali na mtima wabwino.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Acicepele—Kodi Mukukula Mwauzimu?
Yesu anapeleka citsanzo cabwino kwambili pa nkhani yotumikila Yehova na kulemekeza makolo ake.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Makolo Thandizani Ana Anu Kuti Apambane
Mungathandize ana anu kukhala atumiki a Mulungu okhulupilika mwa kuwaphunzitsa pa mpata uliwonse umene mwapeza.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Kanizani Ziyeso Mmene Yesu Anacitila
Ni cida camphamvu citi cimene Yesu anaseŵenzetsa kuti asagonje ku mitundu itatu ya ziyeso zimene anakumana nazo?
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Pewani Misampha Poceza ndi Anthu pa Intaneti
Mofanana na zida zambili, mawebusaiti ocezelelapo pa intaneti angakhale othandiza kapena owononga. Tingaseŵenzetse mfundo za m’Mau a Mulungu kuti tidziŵe zimene zingativulaze na kuzipewa.