June 18-24
LUKA 2-3
Nyimbo 133 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Acicepele—Kodi Mukukula Mwauzimu?”: (10 min.)
Luka 2:41, 42—Yesu anapita ku cikondwelelo ca Pasika pamodzi na makolo ake (“makolo ake anali kukonda” nwtsty mfundo younikila pa Luka 2:41)
Luka 2:46, 47—Yesu anamvetsela kwa atsogoleli acipembedzo na kuwafunsa mafunso (“kuwafunsa mafunso,” “anadabwa kwambili” nwtsty mfundo zounikila)
Luka 2:51, 52—Yesu “anapitiliza kuwamvela” makolo ake, ndipo Mulungu komanso anthu anamukonda kwambili (“anapitiliza kuwamvela” nwtsty mfundo younikila)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Luka 2:14—Kodi vesiyi itanthauza ciani? (“ndipo pansi pano mtendele pakati pa anthu amene iye amakondwela nawo,” “anthu amene iye amakondwela nawo” nwtsty mfundo zounikila)
Luka 3:23—N’ndani anali tate wa Yosefe? (wp16.3 peji 9 mapa. 1-3)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Luka 2:1-20
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Ndiyeno, yankhani pa zimene anthu a m’gawo lanu amakamba posafuna kulalikidwa.
Vidiyo ya Kubwelelako Kaciŵili: (5 min.) Tambitsani na kukambilana vidiyoyi.
Nkhani: (6 min. olo kucepelapo) w14 2/15 mapeji 26-27—Mutu: N’chifukwa Chiyani Ayuda a M’nthawi ya Yohane M’batizi “Anali Kuyembekezera” Mesiya?
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Makolo, Thandizani Ana Anu Kuti Apambane”: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Sanalekelele Mwayi Uliwonse wa Utumiki.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 25
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 17 na Pemphelo